Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




YONA – MNENERI WA CHITSITSIMUTSO!

JONAH – THE PROPHET OF REVIVAL!
(Chichewa)

Ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.
Mbusa Emeritus

Ulaliki wolalikidwa pa Chihema cha Baptist ku Los Angeles
Chakumadzulo a tsiku la a Mbuye, Juni 14, 2020
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, June 14, 2020

“Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti, Nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nularikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga” (Yona 1:1, 2).


Buku la Yona linayenera kulembedwa ndi mneneri Yona mwini. Ndanena ichi chifukwa likuulula maganizo ndi mapemphero, oti wina sanganene kuposa iye mwini angadziwire. Zoona ndizoti Yona ndi wa mbiri yakale zaonetseredwa pa II Mafumu 14:24-25. Pamene alembi akale anamutchula iye, “Yona mwana wa Amitai, mneneriyo, ndiye wa Gati-heferi” (II Mafumu 14:25). Ambuye Yesu Kristu mwini analankhula za Yona kuti anali weni-weni wa mbiri ya kale. Chonde tsekurani Mateyu 12: 39-41. Imani pamene ndikuwerenga za mmene Yesu ananenera za Yona,

“Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa achigolo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri [Yona]: Pakuti monga Yona anali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wache, chomwecho mwana Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wache. Anthu aku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwacha kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano” (Mateyu 12:39-41)

Imanibe ndipo tsekulani Luka 11:29-30

“Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikilo, ndipo chizindikilo sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikilo cha Yona. Pakuti monga ngati Yona anali chizindikilo kwa a Ninevi, chotero adzakhalanso Mwana wa munthu kwa m’badwo

Mukhoza kukhala.

Ndiye II Mafumu 14:25 akutipatsa mbiri ya Yona. Ndi Luka 11:29-30 Yesu akutionetsa Yona ngati chizindikiro. Ndipo Mateyu 12:39-41 tikuonetseredwa kuuka kwa Yona ngati chizindikiro cha kuikidwa m’manda ndi kuukanso kwake pa tsiku la chitatu ataikidwa m’manda. Kotero chipangano cha kale chikunena za Yona ngati munthu weni-weni, ndi Kristu mwini akutiuza kuti infa ya Yona ndi kuuka kwake unali uneneri wa infa ndi kuukanso kwa Kristu mwini.

Bambo Winston Churchhill ananena bwino motere, “Tikanali wosakhulupirira ndi maganizo a chilendo a Gradgrind ndi Dr. Dryasdust. Tikhonza kukhulupirira kuti zinthu zinachitika monga m’mene zinakhazikitsidwira mzolembedwa zoyera za [Baibulo].” (Zokoperedwa ndi Dr. J. Vernon McGee, Kumasulira Baibulo lonse voluyumu III, onani m’mene amufotokozera Yona, tsamba 7380.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

I. Choyamba, maitanidwe a Yona.

“Ndipo mau aYehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndikuti, nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nulalikire motsutsana nao…” (Yona 1:1,2)

.

Vesi 3,

“Koma Yona ananyamuka kuthawa…kuzemba Yehova” (Yona 1:3)

Ndimamumvetsetsa munthu ameneyu wotchedwa Yona. Ndi chifukwa chache buku ka Yona ndilimodzi a mabuku amene ndi mawakonda a mchipangano cha kale. Yona anathawa pamaso pa Ambuye. Ine sindinachite zimenezi. Ndinaitanidwa kukhala wa mishoni ndipo ichi ndikuchidziwa. Koma ndinali mwana wa sukulu wosauka ndipo ndimadziwa kuti sindinga malize sukulu. Ndinayenera kuti ndimalize sukulu kuti ndikhale wa mishoni wa Baptist. Komabe ndimamva ngati Yona. Ndimamva kuti ndaitanidwa, koma ndimayesa kuthawa Mulungu pochita mantha kuti mwina sindikhoza mayeso a kusukulu. Mulungu amandiuza kuti ndichite chinthu china chosatheka.

Mwana wa sukulu mzanga anandiuza kuti, “sindingapite muutumiki chifukwa ndi kuopa kuti zikandibvuta ndi kusiya utumika.” Amaopa kuti adzalephera mu utumiki. Ndinachiganizira chinthu ichi kwambiri. “Ine ndimafuna kuzisiya kale koma sindiwopanso.

Mantha amapangitsa kuti munthu woitanidwa ndi Mulungu a thawe maitanidwe ake. Amakhala mantha mnjira imodzi kapena inzake. Mnyamata uyu amachitabwino mzonse zomwe amachita – koma amaopa kulowa mu utumiki. Mng’ono wake anati za iye, “Mbale wanga akhonza kuchita chirichonse.” Koma amalephera kumasuka ku mantha “akuti adzalephera mu utumiki.” Anali wamtali, manja asanu ndi limodzi, ndipo anali ndi mphatso yolarikira bwino. Koma anathawa pa maso pa Ambuye chifukwa cha mantha!

Tsopano ndifuna ndikuuzeni chinachake achinyamata chimene ndaphunzira m’moyo uno, “ukhonza kuchita chirichonse chimene Mulungu wakuitanirani kuchita – chirichonse!” Baibulo limati, Ndikhonza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13). Pakuti ndinaliyesa vesi limeneri, ndipo ndikudziwa kuti ndi lowona. Taona pano ndiri ndi zaka 80 za moyo, wochira ku nthenda ya khansa, bondo langa lodwala, koma sindiopa, chingakhale anthu a wiri oyipa anatenga gawo lalikulu la mpingo pa nthawi ya mpatuko wa ukulu. Komabe ndine wodekha ngati khanda m’manja mwa mai wanga. Ndikuopa ngati? Zoona zake ndi zakuti sindikuopa ndi pang’ono pomwe! A mai anga ondibereka ankakonda kundiuza kuti, “ulibe choti ungaope koma umaopa mantha” Izi anazimva kuchoka kwa Pulezidenti Franklin D. Roosevelt nthawi ya chipsinjo chachikulu. Ndipo ndi nazindikira kuti agogo anga amanena zoona!

Ndinazindikiranso kuti munthu sungathawe “pamaso pa Ambuye.” Chifukwa ninji? Chifukwa Mulungu amapita nawe kuli konse ungapite – chifukwa chake! mutha kuthawa, monga m’mene Yona anachitira, anapita ku Tasisi. Koma Mulungu analiko kumeneko monga analiri kumudzi! Ndipo Mulungu sadzalola kuti mlaliki adutse mopanda mabvuto .

Ndikukumbukira munthu wina amene anali chiledzerere. Ndinazindikira kuti amamwa kuti asamve maitanidwe a Mulungu akamamuitana, anali ndi mantha akulu kuti amvere maitanidwe a Mulungu. Dzina lake anali John Birch (sizabodza izi!) tinali limodzi kusukulu, amakonda kumathawira kupita kunja kukamwa!

Ndinadziwa bambo wina wotchedwa Alan. Ndinamutengera Alan kwa Kristu, koma sizinali zophweka. Chifukwa ninji, Alan anali ndi mantha kuti ngati wapulumutsidwa adzapita Kumwamba! Kodi amaoperanji kupita Kumwamba? Tsiku lina anandiuza kuti, “Ndikuopa kukakumana ndi bambo anga chifukwa ndinakana kupita ku sukuku ya ubusa kuti ndidzakhale mlaliki wa chi presibetere ngati iwowo.” Alan anali ndi zaka zoposa makumi asanu ndi limodzi. Anali mkachisi wa purezibetere tsiku la Mulungu, wamantha kuti apulumuke chifukwa malemu bambo ake akakwiya naye akakapezana Kumwamba! Malingaliro amenewa anamsautsa kwa zaka makumo anayi. Koma ndinayesa kumulimbikitsa kuti malemu bambo ake [Abusa Black] akamwetulira ndikumukumbatira akakamuona, ngati zija zinachitika ndi mwana wolowerera, pamene anabwerera kwa bambo ake. Alan anali munthu m’modzi amene ndinamutengera kwa Kristu!

Ndiri ku sukulu ya ubusa, mwana wasukulu mzana mtsikana anapulumutsidwa pa nthawi ima ya mapemphero. Anali mtsikana wa manyazi, koma ndinazindikira kuti anali wobvutika m’maganizo, ndinakalankhula naye. Anati “ ndikuchita mantha kuti ndiwauze amai anga kuti ndapulumutsidwa.” Ndinamuuza kuti akawauze palibe choipa chimene akachite,” Koma sizinali choncho. Atamva mai ake kuti wapulumutsidwa, anamuthamangitsa panyumba pao. Ndinamuona akulira. Ndinati, “undilore ndipete ndikakumane nao amai ako.” Ndinavala bwino ndi tayi yanga pakhosi kukakumana nao mai ake. Atadziwa kuti ndine ndani, anayamba kundilalatira. Kenaka ndinalowa pa chipinda chochezera, ndinati, “kodi simungamulore mwana wanu kuti abwere kunyumba?” Ndipo anati, “Ndinkalolera kuima naye pamene amamwa mowa ndikuchita za chiwerewere, koma tsopano pakuti ndi mkristu! Sindikumufunanso mnyumba mwanga muno!

.Momvetsa chisoni mtsikana uja anakakhala kunyumba kwa anzake opemphera nao, kenaka anapeza ntchito, ndikumaliza maphunziro ake. Kenaka anakwatiwa ndi mnyamata wabwino. Ndinamvetsedwa kuti mai ake sanabwere ku ukwati wake. Banja lija linapita kukakha a mishoni ku dziko lina la ku ulaya. Timawatumizira ndalama mwezi ndi mwezi zowathandizira pa utumiki wao.

Tsiku lina ndinangomva kuti manyuzi anaunjikidwa pakhomo pao, kusonyeza kuti wa mkati mwa nyumbayo samazitenga. A polisi anaphwasula chitseko ndikupeza kuti maiwo anali - atafa – kumanja kwao kuli velemoti la mowa! Zachisoni kwambiri.

Oh, mtsikana uja anadutsa mzowawa ndi misozi kuti akhale m’Kristu ndi wa mishoni! Koma anamukonda Yesu koposa nagonjetsa mantha ndi kumutsatira mpaka kukafika kukakhala wa mishoni! Ndipo anamvera zimene Yesu amamuuza,

Imani tsekulani Baibulo lanu pa Mateyu 10:34-39.

“Musalingalire kuti ndinadzera kudzaponya mtendere pa dziko la pansi; sindinadzera udzaponya mtendere, koma lupanga. Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wache, ndi mwana wa mkazi ndi amache, ndi mkazi wokwatiwa ndi apongozi ache: ndipo apabanja ache a munthu adzakhala adani ache. Iye wakukonda atate wache, kapena amache koposa Ine, sayenera Ine, ndipo wakukonda mwana wache wa mwamuna, kapena wamkazi kuposa Ine, sayenera Ine. Ndipo iye amene satenga mtanda wache, natsata pambuyo panga, sayenera Ine. Iye amene apeza moyo wache, adzautaya, ndi iye amene ataya moyo wache, chifukwa cha Ine, adzaupeza.” (Mateyu 10:34-39)

Mukhonza kukhala.

Ndikudziwa kuti ena a inu makolo anu adzayesetsa kuti muchoke mu mpingo wathu muno. Chonde kumbukirani za kulimba mtima kwa mtsikana uyu ndikutengapo chitsanzo. Mukatero, adzakupserani mtima – kwa kanthawi. Koma akadzaona moyo wanu wabwino, mapeto ake – kutsogoloku – adzabwera nanu kutchaitchi kuno. Koma muyenera kukhala ndi chikhulupiriro kutsatira Kristu, chingakhale atakukanani kotheratu! Musakhale ngati Yona ndi kuyesa kuthawa Ambuye!!!

Ku mpingo wa chi China, ndinali ndi azanga awiri – amatchedwa Ben ndi Jack. Ben woukira motsutsana ndi Dr. Lin. Kenaka anathawitsana ndi kachibwenzi kake. Sindinawaonenso. Koma Jack anaphunzira za mankwala. Koma sanazikonde, kotero anapita kusukulu ya ubusa ya Talbot na khala mlaliki. Anali mzanga kwambiri. Ndinali woyimanaye pa ukwati wake. Anakhulupirira Yesu pa umodzi wa misonkhano yathu. Kenaka analemba motere, “Patatha zaka za mbiri izi zinapindula zipatso za chipulumutso cha Bambo ndi Mai wanga… Ndinachitira umboni bambo anga ndi kuwaphunzitsa mpakana kumatumikira ngati mphunzitsi wa maphuziro a la sabata. Kukhudza miyoyo ya ophunzira awo ndi kuthandizira pa kukula kwa mpingo.”

II. Kachiwiri, Kunzunzika kwa yona.

“Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzembera Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisi, napereka ndalama zache, natsikira m’menemo, kuti apite nao ku Tarisi kuzemba Yehova. Koma Yehova anautsa chimphepo chachikuru pa Nyanja, ndipo panali namondwe wamkuru panyanja, ndi chombo chikadasweka.” (Yona 1:3-4)

Taonani, Yona amadziwa kuti namondwe ndi wochoka kwa Mulungu.

“Ndipo anati nawo, mundinyamule ndi kundiponya m’nyanja, momwemo Nyanja idzachitira inu bata, pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkuru amene wakugwerani chifukwa cha ine” (Yona 1:12)

.

Pamaliza amalinyero anatena Yona ndi kumuponya m’nyanja, ndipo Nyanja inachita bata.

“Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikuru chimeze Yona. Ndipo Yona anali m’mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku. Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m’mimba mwa nsombayo” (Yona 1:17-2:1)

.

Poyamba zinali zondibvuta kuti ndikhulupirire ichi. Koma kumapeto ndinazindikira kuti zimalunjika kwa Yesu, amene anafera pa mtanda, naikidwa m’manda, kenaka ndi kuuka kwa akufa.

Kenaka ndi nadzawerenga zomwe Dr. M. R. DeHaan ananena za Yona ndi chinsomba chachikuru. Dr. DeHaan anati Yona anafa mkati mwa chisomba chachikuru. Dr. J. Vernon McGee anati,

Buku iri ndi la uneneri wa kuukanso kwa akufa. Ambuye Yesu Mwini anati monga Yona anali chizindikiro kwa a Nenive, Iye adzakhala chizindikiro ku mbadyo Wake mu kuuka kwake kwa a kufa… Kabuku kakang’ono ka Yona kamaonetsera ndi kuphunzitsa za kuuka kwa akufa kwa Ambuye Yesu (Zolembedwa mu Kusanthula Baibulo lonse, zokhudzana ndi kuuka kwa a kufa, voluyumu III. Tsamba 739).

Taonani Yona 1:17.

“Koma Yehova anikiratu chinsomba chachikuru chimeze Yona. Ndipo Yona anali m’mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku” (Yona 1:17).

Tsopano taonani mau ofunikira kwambiri m’Buku la Yona, mau asanu omalizira a Yona 2:9,

“Chipulumutso n’cha Yehova” (Yona 2:9b)

Ndiime kaye pano kuti ndipereke maganizo anga za masautso a Yona m’chisomba chachikuru.

Pamene ndimawerena Buku la Yona usiku wina, ndinakhudzidwa ndi china chake chomwe sindinachiganizepo chikhalire. Nzachidziwikire kuti chitsitsimutso “Chimabutsidwa” ndi zimene tikudutsamo. Alaliki ambiri akuti Kolona Vailusi “abutsa” chitsitsimutso. Ine sindikukhulupirira zimenezi mpang’ono pomwe!!! Awa ndi maganizo a Finney, ndipo sioona nkomwe.

Zeni-zeni za chitsitsimutso ndi izi – chima “butsidwa” (Ndimadana ndi mau amene a laliki amasiku ano akunena) – chitsitsimutso “chimabutsidwa” ndi Mulungu Mwini, “Chitsitsimutso ndi cha a Mbuye’ (Yona 2:9b)

Koma ichi ndi chimene ndinaona usiku wina – Powerenga za mbiri ya chitsitsimutso chachikuru, timapeza kuti zitsitsimutso zambiri zimayamba ndi pamene atsogoleri akudutsa m’manzunzo. Nditchulapo ochepa amene ndawakumbukira.

John Wesley – Ndikungofuna nditolepo manzonzo angapo amene anakumana nao chisanafike chi Tsitsimutso choyamba. Anali wolephera ngati wa mission ku Georgia. Anakangana ndi ziwanda. Analipafupi kuotchedwa chifukwa chodananaye. Anali pafupi kumwalira. Mzake George Whitefield anasiya kuyenda naye. Ananyozeka ndi mpingo wake womwe. Ananyozedwa mumpingo wa abambo wake ndi kukanidwa kuti asadye mgonero ndi mbusa. Anakwatira mkazi wolalata amene mapeto ake anamuthawa. Kenaka Wesley anakumana ndi Pentekositi yake. Pamenepo ndi pamene anakumana ndi Pentekosite yake! Zikwi-zikwi za anthu zinadza kumva ulaliki wake. Ulaliki wake unamveka ponse-ponse. Ntchito yake ndi uliliki wake anatchulidwa ndi akulu- akulu a mfumu: “Panalibe munthu m’modzi amene anatakasa malingaliriro a anthu ambiri. Panalibe liu limodzi limene linakhudza mitima ya anthu ambiri. Panalibe munthu wina amene anakhudza miyoyo mu England.” Wosindikiza mabuku wina posachedwapa anati, kuti John Wesley anali “m’modzi mwa alaliki a mphamvu kuyambira nthawi ya Apositoli.”

Marie Monsen – Anayamba kusala ndikupempherera chitsitsimutso cha China. Satana anamkokera pansi ndi kumupinda-pinda ngati chinjoka chachikulu. Anapitiriza kutumikira popanda thandizo liri lonse munthu wa mai kulimbana nao yekha utumiki, amene anapempherera chitsitsimutso kufikira lero lino chiri m’manyumba a mbiri ku China,

Jonathan Goforth – Iye ndi mkazi wake anapita ku China kumene anakanzunzika kwambiri. Anayi mwa ana awo anamwalira. Bambo Goforth mwini anali pafupi kufa kawiri konse. Ananyamulira ana ake akufa mngolo ndi kuyenda maola 12 kuti akaikidwe ndi mwambo wa chi Kristu. Ndikanakonda ndikanakhala ndi nthawi kuti ndikuuzeni m’mene mkazi wa Goforth ndi ana ake ananzunzikira. Pamene mwana wawo Constance anamwalira, “Thupi la khanda lathu Constance linaikidwa pafupi ndi manda a mulongo wake pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Okutobala 13, 1902.”
     Apa ndi pamene moto wa chitsitsimutso unabuka m’misonkhano ya Goforth. Mwai unapatsidwa wa mapemphero. Mkazi wa Goforth anati, “Chinabwera mwa dzidzi ngati mphamvu ya mphenzi…chinafika chifukwa cha mphamvu ya ma pemphero. Panalibe amene akanaletsa kapena kuyesa kutero… ena amene anamusiya Mulungu, tsopano ayamba kubwerera, ndikulapa machimo awo poyera… Panalibe chisokonezo. Mpingo wonse unagwirana manja m’pemphero…timapita kumapemphero tiri pa maondo athu, izi zinari zosangalatsa kwambiri ndi zopereka ulemerero! Tinawerama pansi ndi kumva mau a Mulungu akuti, ‘khala chete dziwa ine ndine Mulungu.’ Tsopano taphunzira kuti ‘si mphamvu, si nkhondo, koma Mzimu wa Ambuye wa makamu.’
      “Gulu lambiri, kuposa 700, anathinikana patsogolo kulapa machismo awo… Kunali kobvuta kuti titseke msonkhano. Msonkhano uliwonse umatha maola atatu. Msonkhano uliwonse nthawizina umatha tsiku lonse la thunthu… Goforth amapereka uthenga wa ufupi kuwatsimikizira anthu pa chisankho chomwe achita kuti kuli moyo wina wabwino. Awatu anali ma Puresbetere a mphavu, amene amalira kwa Mulungu kuti awachitire chifundo… Mlaliki wa chi Puresibetere m’modzi anapezeka kumapeto kwake, anali m’kachipinda ka yekha, akulirira movutika ndi mtima.” Mkazi wa Goforth anati, “Mapemphero otere ndi a chindunji, ophweka, ndi a chiyembekezo! Chinali chirimbikitso kupezeka munthawi ngati imeneyi!”
      “Amishoni a chizungu limodzi ndi abale a chi Chinese anabvomereza kulakwitsa, ndi machimo awo. Inali nthawi yoyika zinthu pamodzi – munthu wa chi China ndi wa chi China, wa mishoni ndi wachi China, izi zonse zinatheka chifukwa analumikizidwa pamodzi ndi Kristu. Ndipo Yesu amati kwa ife tonse, ‘kuti onse akhale amodzi… Ine mwa iwo ndi Inu mwa Ine, kuti wonse akhale angwiro mu umodzi.’”

Tinali ndi misonkhano ku mpingo wathu wakale umene umaoneka kunja ngati misonkhano ya Dr. Goforth ku China. Ndanena dala zakuti “kunja.” Koma ambiri mwa “atsogoleri” athu anamunamiza Mulungu pamene amalapa machimo awo. Monga, Dr. Tozer anati, anthu amenewa anachita machimo awiri – tchimo la bodza, ndi tchimo lonama mdzina la Mulungu! Kreighton anamunamiza Dr. Cagan pamene ananena kuti sakufuna “kulalika” kuti “akwaniritsidwe.” Kotero mnyamata womvetsa chisoni uyu anakhala ngati Yudasi, amene anampereka Kristu, kuposa Petro amene analapa zeni-zeni.

Chitsitsimutso cheni-cheni chomwe chinali ndi Jonathan Goforth chinafanana ndi chitsitsimutso cheni-cheni chomwe ndinachiona chochitika ndi Dr. Timothy Lin, ku mpingo woyamba wa Baptist cha mzaka za 1960, kumene samakhazikika pakunena za “mphatso za Mzimu” – koma kulapa ndi pemphero zokha. Mwachisoni, zikuoneka ngati kuti “kutsutsika ndi kulapa” kumene kumachitika sikunali kweni-kweni kochoka pansi pa mtima. Zikuonekabe kuti anthu monga Kreighton ndi Griffith amaganiza kuti akhonza kumupusitsa Mulungu!!! Ndi khungu lanji lotere!!!

Pamene ndimalemba ulaliki uwu kuchipinda kwanga kosambira mausiku ochepa apitawo, ndina khala mphepete mwa chosambira. Kanthawi kena kake ndinagwa chagada kugwera mosambiramo, ndimaganiza kuti ndamenyetsa mutu wanga m’chosambiramo. Ndinali chigonere cha gada miyendo iri m’mwamba. Ndinayesa kudzivuula koma ndinalephera. Ndiri chigwere choncho, ndimaganiza kuti ndatyola khosi langa. Kenaka ndinaona kuti khosi liribwino.

Ndikanali chigonere mosambiramomo, Satana anandiuza kuti sikudzakhala chitsitsimutso cheni-cheni. Ndipamene Mulungu anandisonyeza kuti chitsitsimutso chachikulu chinadza ndi anthu monga Wesley, Marie Monsen, ndi Jonathan Goforth, ndi ena monga John Sung, iwowa anadutsa m’mayesero akulu, monga Yona m’mimba mwa somba yaikulu, Mulungu asanawakhulupirire ndi chitsitsimutso chimenechi. Kodi chitsitsimutso cheni-cheni tikhonza kukhalanachonso panopa? Mwina. Tiyenera kukhala woona mtima ndi wokhulupirika, apo ayi Mulungu sangatumizenso chitsitsimutso cheni-cheni chimene ena aife takhala tikupempherera zaka zonsezi.

Monga Yona, Mbusa Richard Wurmbrand anali m’mimba mwa somba zaka 14 mndende ya chi Komonisiti. Zaka zitatu mwa 14 zimenezi anali mkachipinda kayekha, osawona wina aliyese koma onzunzawo. Ndi chifukwa chiani Mulungu analola kuti Wurmbrand adutse mu zonsezi? Mukawerenga buku lake mudzaona kuti Mulungu anagwiritsa ntchito kachipinda ka ndendeyo kumuphunzitsa kuti akhale wa chikondi ndi woona mtima. Sindinakumane ndi munthu woona mtima ngati Richard Wurmbrand. Anahunzira kunena chilungamo chokha-chokha nthawi imene anali mmdende, chomwe atamasulidwa anachilalikira kudziko lonse la pansi. Anyamata monga Kreighton ndi Griffith sanali woona mtima. Mpaka anafika pomunamiza Mulungu. Ananamizira “kulapa” machismo chinthu chomwe sichinali tanthauzo kwa iwo.

Ndi chapafupi kuona John Wesley, Marie Monsen, ndi Jonathan Goforth kuti anali anthu otsimikiza mtima, osati ongoyerekeza. Umu ndim’mene analirinso Yona.

Dr. A. W. Tozer anati, “Ngati ndife wopusa, tikhonza kumangotaya nthawi kupempha Mulungu kuti atumiza chitsitsimutso, pomwe sitikutha koona zoyenereza ndikumango pitiriza kuphwanya malamulo Ake. Kapena kuyamba panopa kumvera ndi kuphunzira mdalitso wopezeka chifukwa cha kumvera. Mau a Mulungu ali patsogolo pathu. Tiyenera uwerenga ndikuchita zimene akunena ndipo chitsitsimutso...chidzabwera monga kholola limabwera pofesa ndi kubzala” (“What About Revival? – Gawo I”). Kuona mtima ndi chimene Mulungu akufuna!


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo


KALEMBEDWE KA

YONA – MNENERI WA CHITSITSIMUTSO!

JONAH – THE PROPHET OF REVIVAL!

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.

“Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti, Nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nularikire mutsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga” (Yona 1:1, 2).

(II Mafumu 14:25; Mateyu 12:39-41; Luka 11:29-30)

I.   Choyamba, maitanidwe, a Yona, Yona 1:1,2,3; Afilipo 4:13; Mateyu 10:34-39.

II.  Chachiwiri, Kunzunzika kwa Yona, Yona 1:3-4, 12; 1:17-2:1; 1:17; 2:9b.