Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.
Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.
Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.
Nyimbo yoyimbidwa ulaliki usanayambe: “Ndine Msirikali wa Mtanda?”
(ndi Dr. Isaac Watts, 1674-1748).
KUPACHIKIDWA NDI KRISTU!CRUCIFIED WITH CHRIST! ndi Dr. R. L. Hymers, Jr., “Ndinapachikidwa ndi Kristu: koma ndiri ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao tsopano m’thupi, ndiri nao mchikhulupiriro cha mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine” (Agalatiya 2:20). |
Kodi zimatanthauza chiyani “kupachikidwa ndi Kristu”? Ndikukhulupirira zimatanthauza kuti tiyenera kupita ku nthawi ya mdima ya moyo wathu. Tiyenera kuumva ululu wa machismo athu, kumva kupyeteka kwa lamulo, kuimva misumali, kufa ndi Kristu- kulumikizana ndi Kristu mu infa Yake, komanso kuuka kwake.
Mbusa Richard Wurmbrand anapachikidwapo ndi Kristu pamene anali mu ndende, malo ayekha kwa zaka ziwiri. Mu buku lake, Malo a Mulungu a Chinsinsi, (In God’s Underground), amalongosola m’mene anapachikidwira ndi Kristu. Wurmbrand anati,
Ndinasungidwa malo a ndekha mchitokosi kwa zaka ziwiri. Ndinalibe chowerenga ndi polembapo; ndimango sinkha-sinkha ndekha m’maganizo, chinthu chomwe sichinandichitirepo.
Kodi ndimakhulupirira Mulungu? Tsopano mayeso anandipeza. Ndinali ndekha. Panalibe malipiro ena aliwonse, popanda mwai woti ndikhonza kulingalira. Mulungu amangondipatsa manzunzo – kodi ndipitiriza kumutsatira?
Pang’ono-pang’ono ndinayamba kuzindikira kuti pa mtengo wa chete panalendewera chipatso cha mtendere… ndinazindikira kuti chingakhale muno [m’malo andekha] malingaliro anga anapotolokera kwa Mulungu, kuti ndi nakhalira kupemphera usiku wina uliwonse, kudzirimbitsa mu uzimu komanso matamando. Ndinadziwa tsopano kuti awa sianali masewera. NDINAKHULUPIRIRA! (Malo a chinsinsi a Mulungu, tsamba 120).
+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.
+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
Kodi zimatanthauza chiyani “kupachikidwa ndi Kristu”? Ndikukukhulupirira zimatanthauza kuti tiyenera kupita ku nthawi ya mdima ya moyo wathu. Tiyenera kuumva ululu wa machismo athu, kumva kupyeteka kwa lamulo, kuimva misomali, kufa ndi Kristu- kulumikizana ndi Kristu mu imfa Yake, komanso kuuka kwake.
Kawiri-kawiri anthu amakani ngati ine tiyenera kudutsa mu izi kambiri-mbiri tisanagonje ndi “kupachikidwa ndi Kristu.” Ndikadaphunzirabe za zoona izi, chingakhale tsopano ndiri ndi zaka makumi asanu ndi atatu amoyo.
Ndinayamba kuphunzira za zoona izi pokhala mu mpingo wa chi Tchaina, kumenene ndinali “wa kunja” kwa zaka zambiri. Ndimafuna kuchokamo, koma Mulungu sanalore kuti ndichoke. Anandiuza mwa chimvekere kuti ndisachoke pa Ahebri 10:25 ndi malo ena m’baibulo. Pamenepo ndi nayamba ku “pachikidwa ndi Kristu.”
Nthawi ina imene ndinayesedwa ndi ndi pamene ndinali ku sukulu ya Southern Baptist ku dziko la Marin. Ndi madana nao malo amenewo chifukwa pafupi-fupi aphunzitsi onse anali osatembenuka amene amang’amba Baibulo zidutswa-zidutwa mkalasi iriyonse. Ndimadana ndi kukhala pamenepa, koma, Mulungu anandiuzanso kuti ndisachoke, kaya ndi kuwawa motani. Patadutsa pang’ono pakati pa usiku, m’chipinda change kusukulu komweko, Mulungu anandiitana pakati pa usiku. “Mu mau a yaziyazi” Mulungu anati kwa ine, “Mu zaka zambiri kuyambira pano udzaganizira za usiku uwu ndi udzakumbukira kuti ndinakuuza kuti ntchito yako idzayamba ukadza kalamba…Pamenepo udzaphunzira kuti suyenera kuoopa. Ndidzakhala nawe…Ngati iwe sudzakana palibe amene adzakane, ndipo izi ziyenera kunenedwa - pomwe ena akuchita mantha kunena, kotere ngati iwe sunena palibe amene atanene, mwina ngati anganene sadzanena molondola.”
Ndiye kunalinso mphunzitsi wanga amene amaphunzitsa homiletiki Dr. Gordon Green, amene anati kwa ine, “Hymers, ndiwe mlaliki wabwino kwambiri, m’modzi mwa ochita bwino kwambiri. Koma…. Sudzakhala mbusa wa Southern Baptist ngati susintha kubvutitsa.” Ndinamuyang’ana m’maso ndipo ndinati, “Ngati dipo lake ndi limeneli sindikulifuna.” Palibe chimene ndikuchisowa panopa. (Motsutsana ndi Mantha Onse, tsamba 86) (Against All Fears, p.86)
Kenaka ndinabwera ku Los Angeles kudzayambatsa mpingo umenewu, kenaka Kreighton anaugawa mpingo chifukwa “samagwirizana” nane. Kodi samagwirizananane chiyani? Samagwirizana ndi kulimba mtima kwanga pa zinthu, izi ndi zimene samagwirizana nane! Anali mnyamta wa “manyazi”chabe, wa mantha kuima pa choonadi cha mulungu! Basi ndapita, kamunthu ka mantha iwe!
Tsopano, mzaka za m’ma 80, ndinazindikira kuti Mulungu amandikonzekeretsa konseku kuti ndikhale liu lake la uneneli la m’masiku otsiriza a uneneri. (II Atesalinika 2:3)
Pamene ena akunena kuti tidzakwatulidwa, ine ndikuti muyenera kulowa mu chinsautso Chachikulu, monga Marvin J. Rosenthal amanenera mu Mkwatulo wa mpingo usanachitike mkwiyo. Pomwe ena, monga Kreighton, akuuna kukukokerani ku maulaliki ena, ine ndikuti, “Imani njii mwa Kristu-kaya zibvute bwanji.”
Sindidana naye John Samuel. Ndinangozindikira kuti siwamphamvu kwambiri kukhala liu la uneneri m’masiku otsiriza ano. Amaopa kuti “ adzaphwanyika ndi kupsa.” Akapitirira kukhala ndi ine. Ichi ndichifukwa choti John Samuel sana “pachikidwe ndi Kristu.” Ine ndaphwanyika ndi kupsa” kambiri-mbiri koti sindiopsedwanso!
Dr. Cagan amakonda kundiuza kuti amakonda malalikidwe anga anenena kuti tikhale a mphamvu m’masiku otsiriza ano. Ichi ndichirimbikitso chachikulu kwa ine! Ngati muna “pachikidwa ndi Kristu” mudzapitiriza kukhala ndi ine ndi Dr. Cagan m’masiku a onyoza ano (II Atesalonika 2:3), ndipo mudzakhala wofera chikhulupiriro wa ulemerero- kapena wobvomereza wa ulemerelo, ngati Mbusa Wurmbrand!
“Ndinapachikidwa ndi Kristu: koma ndiri ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao tsopano m’thupi, ndiri nao mchikhulupiriro cha mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine” (Agalatiya 2:20).
Dr. Timothy Lin, m’mbuku lake Ufumu wa Mulungu, anati, “ Masiku ano ma membala ambiri satha kumva liu la Mulungu chifukwa ama dzikonda kusiyana ndi zonse… mitima yawo ndi youma, chingakhale a phunzire motai amankira-nkira kugontha mkutu. Ambiri amaganiza kuti amadziwa kanthu, chonsecho ndi mbuli za zoonadi zambiri.Ambiri a iwo sangakuuzeni cholinga chao cha moyo uno!” Dr. A. W. Tozer anapereka chitsanzo ichi.
Anafunsa mwana wa sukulu ya ukachenjede, Bobu, ali kuno chifukwa chiani?”
“Ndikufuna, Ndikufuna kupanga ndalama, ndiponso ndikufuna kumakayenda maiko ena ndi ena.”
“Koma Bobu, Izi ndi za kanthawi kochepa. Udzazichita ndikukalamba ndi kufa. Cholinga chachikulu ndi chiyani cha moyo wako?”
Kenaka Bobu anati, “ Sindikudziwa ngati ndiri cholinga china cha moyo.”
Anthu ambiri sakudziwa cholinga cha moyo wawo (“Cholinga cha Munthu,” tsamba 27)
M’Kristu akhonza kunena kuti cholinga cha moyo ndi kupita Kumwamba. Koma Dr. Lin anati mobwereza-bwereza kuti kulibe vesi m’malemba lomwe limanena kuti kupita kumwamba ndiye cholinga cha moyo wanu!
Pokuonetserani chomwe ndi cholinga cha moyo, yang’anani II Timoteo 2:12. Werengani gawo loyamba la vesi 12,
“Ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye…”
“Kunzunzika” litanthauzasnso “kupirira.” Chibvumbulutso 20:6 amati, “adzakhala a nsembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwi.” Liu loti “kunzunzika” litanthauzanso “kupirira.” Nfundo imene iri pa II Timoteo 2:12 yaperekedwa pa II Timoteo 2:1-11. Imene ikunena momveka bwino pa vesi 1, “Njira ya ‘msirikari wabwino’ mnthawi yotaya chikhulupiriro.” Kulamulira limodzi ndi Kristu kumeneku kukuonetseredwa bwino mu fanizo la ndalama khumi, pa Luka 19:11-27. Iwo amene akukonzekera kulamulira limodzi ndi Kristu adzapatsidwa “ulamuliro pa midzi khumi” (v.17) kapena “midzi isanu” (v. 19). Dr. Lin anati izi zidzakhala zeni-zeni. Kwa iwo opirira mu moyo uno adzalamulira ndi Kristu mu Ufumu Wake uli nkudza! Liu loti “Kunzunzika” litanthauzanso “kupirira.”
Tsopano tipirire ku chiyani,
“Musakonde dziko lapansi ndi za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chirichonse cha m’dziko la pansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chache, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.” (I Yohane 2:15-17)
Timapirira pakusachoka pamene mpingo ukugawanika,
“Anaturluka mwa ife komatu sanali a ife, akadakha a ife akadakhalabe ndi ife: koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife” (I Yohane 2:19).
Timapirira pakukana kutsatira aphunzitsi onyenga,
“Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu; popeza aneneri onyenga ambiri anaturuka kulowa m’dziko lapansi” (I Yohane 4:1).
Timapirira pakuchita zomusangalatsa Mulungu,
“Ndipo chimene chirichonse tipempha, tipempha kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ache, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pache” (I Yohane 3:22).
Timapirira, pakusunga malamulo a Mulungu,
“Ndipo chimene chirichonse tipempha, tipempha kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ache, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pache. Ndipo lamulo lache ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la mwana wache Yesu Kristu, ndi bkukondana wina ndi mzache monga anatiramurira” (I Yohane 3:22, 23).
Timapirira pamene timvera atsogoleri athu,
“Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu mau a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendendwe ao mutsanze chikhulupiriro chao. Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, asati mwa chisoni: pakuti ichi sichikupindulirani inu” (Ahebri 13:7, 17).
Timapirira pa “pakukhalabe mu ntchito ya Ambuye”- okhazikika!
“Chifukwa chache, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka muntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchita kwanu sikuli chabe mwa Ambuye” (I Akorinto 15:58).
Popirira zinthu izi, Mulungu akutiphunzitsa kukhala akuphunzira , omwe adzalamulire limodzi ndi Kristu mu Ufumu ulinkudza.
“Iye wakulakika ndidzampatsa akhale pansi ndi ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wache” (Chibvumbulutso 3:21, 22).
Mbusa Wang Ming Dao (1900-1991) anakha zaka 22 mndende ku komunisiti Tchaina, chiukwa cha chikhulupiriro chake. Anati,
“Ina anandifunsa kuti kodi mpingo utsate njira iti masiku ano. Ndinayankha musadodoma, njira ya Atumwi… kukhulupirika mpaka ku infa.” Analalikira pa maliro a Dr. John Sung. Mano ake onse anaguluka, anagontha koma anasanduka wakhungu ali mndende momwemo. Atamutulutsa mundende, iye ndi mkazi wake anayamba kuphunzitsa a Kristu mnyumba mwao kufikira infa yake mchaka cha 1991.
Chonde Imani tiyimbe nyimbo yathu,
Ndine msirikali wa m’tanda, Wotsatira mwana wa nkhosa;
Kodi ndidzaopa pakukhala ndi dzina Lake, kapena kukanthidwa polankhula za dzina Lake?
Kodi ndinyamulidwe m’mwamba pa kama wokongola wa bata,
Pomwe ena akulimbirana mphotho, ndi yandama pa Nyanja ya mwazi?
Kodi ndiribe adani olimbana nao? Kodi sindiyenera kukumana ndi namondwe?
Kodi dziko lopanda pake ili bwezi la chisomo, Kundithandizira kunka kwa Mulungu?
Zoona ndiyenera kulimbana, kuti ndikalamulire , onjezerani kulimba mtima kwanga, Ambuye!
Ndidzamva zowawa, ndikupirira zowawa, Ndirimbikitseni ndi Mau Anu.
(“Ndine Msirikari wa Mtanda?” Yoimbidwa ndi Dr. Isaac Watts, 1674-1748).
MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.
(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”
Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo