Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




MAITANIDWE ATHU KUKHALA A MISHONI!

OUR CALL TO BE MISSIONARIES!
(Chichewa)

ndi Dr. R. L. Hymers, Jr.,
Mbusa Emeritus

Uthenga wolalikidwa pa chihema cha Baptist ku Los Angels kumadzulo kwa usiku wa tsiku la Ambuye, Malichi 8, 2020
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Afternoon, March 8, 2020


Yesaya anali, m’mene ndikuonera ine, meneri wamphamvu kwambiri. Koma nanga Yesaya anakhala bwanji kukhala munthu wa Mulungu chomwechi? Mu chaputala cha chisanu ndi chimodzi cha Yesaya, tipezapo yankho.

“Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautari, ndi wotukulidwa, ndi zobvala zake zinadzala m’Kachisi” (Yesaya 6:1).

Yesaya anamva a serafi akufuula kuti, “Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu: dziko lonse la pansi ladzala ndi ulemerero wake” (Yesaya 6:3).

Mnyamata Yesaya Anayikonda Fumu Uziya, fumu yabwino ndi yolemekezeka. Koma tsopano fumu yafa. Chimene chichitike ndi chiyani kwa Yesaya pakuti fumu yafa? Ndikukhulupirira kuti mnyamata ameneyu anamva ngati m’nene enanu mungamvere. Mumamva kupsinjika kuti mpingo wathu watha. Komatu Mulungu anali asanathane naye Yesaya.

Masomphenya awa a Mulungu anakhudza mtima wake . Yesaya sanakhudzidwe mopanda chiyembekezo. M’malo mwake masomphenya a Mulungu anamukhudza mwa njira yina. Anati,

“Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa ; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu”.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Ichi chinali chigonjetso cha uzimu cha mnyamata Yesaya! Nanunso chigonjetso chimenechi mukhonza kukhala nacho. Koma muyenera kufunitsa Mulungu kuposa china chirichonse! Dr. A. W. Tozer anati, “ Anausiya mpingo osati chifukwa samafuna Mulungu – koma pakuti anapeza china chake chimene amachifuna kwambiri kuposa Mulungu… pamene umunthu wao wakale unatakasidwa mwa iwo anamufulatira Mulungu nachoka m’mipingo yawo. Anapalana maubwenzi ndi anyamata ndi atsikana wosadziwa Mulungu. Anapalana maubwenzi ndi dziko lapansi. Analowa zintchito zosawapatsa mpata wopembedzera Mulungu. Anabwereranso kudziko. Anatsimikiza m’mitima yawo kuchita zimene akufuna kwambiri… Ine sindikufuna kuti ndiwapusitse powaphunzitsa kuti akhonza kukhala m’Kristu ndi kukonda dziko lapansi, chifukwa izi sizingatheke. Inde, mukhonza kukhala wonyenga pomalikonda dziko lapansi. Mukhonza kukha m’busa wonyenga polikonda dziko lapansi. Mukhonza kukhala mlaliki wa makono wophweketsa nkumalikonda dziko lapansi. Koma dziwani kuti simungakhale M’kristu weniweni wa Baibulo ndi kumakonda dziko lapansi. Zikhonza kundipweteka moyo ngati ndine ndekha ndikukhulupirira izi, koma sindidzakunyengani posakuphunzitsani” (Ziphunzitso za paguwa za Tozer)

Komanso, Tozer anati, “Koma m’maganizo anga, chosowa chachikulu m’masiku ano ndi mtima wofuma kutumikira, ndipo alariki akhazikike m’masomphenya a Mulungu atakhala pampando wachifumu wautari, ndi wotukuridwa ndi zobvala zake zitadzala m’kachisi.” Popanda masophenya a Mulungu ngati amenewa “timangochita zofuna zathu, nkumachita zinthu zongosangalatsa anthu mtchalitchi…Timaopa kupeputsidwa potero tatsekula khomo la kusowa chipembedzo. Izi zimabweretsa Ngozi ya mu uzimu… zolalikira uthenga wa Mulungu zayamba kuchepa. Zikuchuluka ndi za dziko lapansi mulunjika ku tchimo” (Kutsamira mu Mphepo)

Taonani vesi 5,

“Ndipo ine ndinati, tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa: chifukwa maso anga aona Mfumu Yehova wa makamu” (Yesaya 6:5).

Ndipokhapo pamene mnyamata Yesaya anatsukidwa ndi moto wa Mulungu “ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa” (Yesaya 6:7).

“Tsopano tayang’anani vesi 8. “Ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatumikira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine” (Yesaya 6:8).

Pamene mpingo umagawanikana ndinkaganiza kuti chidwi changa cholalikira chikutha. Ndiye ndinaganiza zokhala usiku wina uliwonse ndi azibambo atatu amene anasiya zao zonse chifukwa cha Kristu – Mbusa Richard Wumbrand, John Wesley, ndi wamishoni womalizira wa ku China, Jonathan Goforth. Awa anali maganizo abwino. Ndinapanga kachipinda kosambira kakang’ono, pafupi ndi chipinda chathu chongona, ngati malo a pemphero ndi chiyanjano ndi azitumika a Mulungu amphamvu amenewa. Kudzera mwa Wumbrand ndinaphunzira kukhazikika, Kudzera mwa Wesley ndinaphunzira kupita chitsogolo pamene mayesero akungotsagana. Koma kudzera mwa Goforth ndi mkazi wake Rosalind, ndinaphunzira kugwa pa maondo mpemphero. Hudson Taylor analemba kalata imene inamutakasa Goforth ndi mkazi wake. Hudson Taylor anati, “ife ngati a mishoni tayesa kulowa mdera lina la China lotchedwa Honan, ndipo tangokwaniritsa posachedwapa. Mbale, ngati ukufuna kukalowa mdela limeneri uyenera kugwa pa maondo.” Mau amenewa ochoka kwa Hudson Taylor anali mau a chirimbikitso kwa Goforth pa utumiki wake wa mdela la kumpoto kwa Honan.

Kenaka mwana wao wakhanda anamwalira. Goforth analemba kuti, “Getuludi wamwalira. Apa tasauka kwambiri. Sabata ziwiri zapitazo anali bwino-bwino, koma pa Julayi 24 anamwalira, patangotha masiku asanu ndi limodzi anadwala nthenda ya m’mimba mwa kamwazi. Ndinanyamula mtembo wake mugaleta pa mtunda wokwana makilomita makumi asanu…kumeneko dzuwa litangolowa ndinakwirira mwana wanga wokondedwa kuti apumule.” Atsikana awiri a chi China amabwera m’mawa wina uliwonse kudzayala nkhata za maluwa pa manda a mwana wathu.

Atatha maliro a Getuludi, Mai Goforth anabereka kamnyamata kokongola. Anakatcha “Khanda Donadi.” Koma tsiku lina khandali linagwa ndi mutu. Kenaka pang’ono pang’ono manja ndi miyendo yake zinayamba kusiya kugwira ntchito. Pa Julaye 25, atangokwana miyezi khumi ndi isanu ndi inayi, Khanda Donadi anamwalira. Kachiwiri Gorforth anakaliyika khanda lake kumanda komwe kuja. Khanda Donadi anayikidwa pafupi ndi manda a mulongo wake, Geturudi. Nthawi yomweyo, pobwerera, Goforth ndi mkazi wake wokondedwa anayamba kukonzekera kupita ku nyumba yawo yatsopano kumpoto kwa Honan. Khanda lawo la miyezi isanu Paulo anapita nawo.

Kenaka mwana wao wina dzina lake Yonatani Goforth anadwala matenda a kaya-kaya. Moyo wake unali pakati pa infa ndi moyo. Pa Junuwale 3, khanda Fulolesi anabadwa. Kunatentha kwambiri koti khanda Paulo anali pafupi kufa, koma anapulumukira mkamwa mwa mbuzi pamene kunayamba kuzizira.

Zowawa ndi zokhoma zambiri zinatsatira. Mwana wao woyamba anafa pa chirimwe. Ana ena awo anamwalira ndi nthenda ya malungo nda nthenda youmitsa khosi. Kenaka Goforth ndi mkazi wake anathawa anthu andewu oukira. Moti panatssala pang’ono kuti aphedwe mozizwitsa.

Mai Rosalind Goforth anagontha makutu. Mwamuna wake ndi amene anali khutu la mkazi wake. Pamene Goforth maso ake anachita khungu, mkaziwake ndi amene anali maso ake. Goforth anafera kutulo pamene mkazi wake anali kosamba ku bafa. Pamaliro pake mwana wake Paulo ananena izi za iye, “Kwa ine bambo anga anali munthu wopambana kwambiri.” Mwana wake wa mkazi Rute anali wa mishoni ku Vietnam. Rute analembera amai ake kalata nati, ndikungoganizira ulemerero umene abambo akupitako… Mulungu wangowakweza ku utumiki wina wa pamwamba.”

Buku lotchedwa, Goforth wa ku China, linalembedwa ndi mkazi wake Rosalind atangomwalira mwamuna wake. Rosalind Goforth anali wa mishoni weni-weni!

Anakumana koyamba pamene anayang’ana mu Baibulo lake, “Ndinapeza lakutha kwambiri, ndi lolembedwa-lembedwa kuchoka ku chikuto mpaka chikuto.” Rosalind anati, “Ameneyu ndiye mwamuna ndingafune kukwatirana naye.” Ndipo anati kwa iye, kodi ukhonza kulumikiza moyo wako ndi ine pa ulendo wa ku China?” Yankho lake linali loti “Inde.” Patangotha masiku ochepa anatinso kwa iye, kodi ukulonjeza kuti udzandilora kuika Ambuye ndi ntchito yake patsogolo, kuposa iwe?” Anamuyankha kuti “Inde” ndidzalola, nthawi zonse.” Samadziwa dipo lake la lonjezano limenero!

“Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatumikira ife, Ndipo ine ndinati, ndine pano; munditumize ine” (Yesaya 6:8).

Tchalitchi lathu lataya anthu amene sanali ndi chidwi chokhala a mishoni. Ndipemphero langa kuti aliyese amene ali muno madzulo ano akhale wa mishoni. Tidzakhala ndi nthawi yobvuta kwambiri kuti tisonkhanitse chuma choti intaneti ya mishoni ipitireze. Inu ndi ine tikhoza kukhala wa mishoni kudziko lonse la pansi mjira ya (1) Kupindula miyoyo; (2) Kupempherera mautumoki athu a mishoni a dziko lonse la pansi; Kupereka ndalama mwezi ndi mwezi zothandizira utumiki wathu wa intaneti potumiza ma ulariki, kuphatikizapo uwu mukuuwerengau, pothandizira amishoni amene ali padziko lonse la pansi m’maiko okwera kumene kularika Uthenga. Wa mishoni wina ananenapo za mwai umenene tirinao masiku ano, “ Tiyenera kukha a Kristu adziko lonse la pansi wokhala ndi maganizo olarikira dziko lonse la pansi pakuti Mulungu wathu ndi wa dziko lonse lapansi.” Kodi mungayankhe ngati muja anayankhira Rosalind Goforth, “Inde, Ndidzalora, nthawi zonse”?

Dzazani masomphenya anga onse, Mpulumutsi, Ndikupemphera, Ndione Yesu yekha lero;
Chingakhale ndiyende mchigwa Munditsogolera, Ulemerero wanu wosaguga undizinga.
Dzadzani masomphenya anga onse, Mpulumutsi, Kufikira kudzera mu ulemerero wanu mzimu wanga udzawala.
Dzazani masomphenya anga onse, kuti chithunzi chanu chionekere mwa ine ndi onse.
Dzazani masomphenya anga onse, Khumbo lonse likhale pa ulemerero Wanu; moyo wanga wotsitsimuka,
Ndi chikondi chanu changwiro, choyera, Kusefukira ndi kuwala panjira yanga kuchoka m’mwamba.
Dzadzani masomphenya anga onse, Mpulumutsi, Kufikira kudzera mu ulemerero wanu mzimu wanga udzawala.
Dzazani masomphenya anga onse, kuti chithunzi chanu chionekere mwa ine ndi onse.

Dzazani masomphenya anga onse, tchimo lisapezeke mwa ine chifukwa cha kuwala kwa mkati mwanga
Ndione nkhope yanu yodalitsika yokha, dyetsani moyo wanga ndi chisomo chosatha.
Dzadzani masomphenya anga onse, Mpulumutsi, Kufikira kudzera mu ulemerero wanu mzimu wanga udzawala.
Dzazani masomphenya anga onse, kuti chithunzi chanu chionekere mwa ine ndi onse.
(“Dzazani masomphenya anga” “Fill All My Vision” ndi Avis Burgeson Christiansen, 1895-1985).


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo