Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.
Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.
Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.
MISOZI MPEMPHEROTEARS IN PRAYER Ndi Dr. Christopher L. Cagan “Ameneyo, m’masiku a thupi lache anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kupulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa” (Ahebri 5:7). |
Mutu wathu ukulankhula za Yesu akupemphera m’munda mwa Gethsemane, usiku uja asanapachikidwe. Anali wopsinjika pakuti machimo athu anaikidwa pa Iye, kuti awanyamule mthupi lake pa mtanda pa tsiku lotsatira. Uthenga wabwino wa Luka ukutiuza,
“Ndipo pokhala Iye m’chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho akulu a mwazi alinkugwa pansi” (Luka 22:44).
Kristu anapemphera “ mu ululu wa ukulu” usiku umenewo. Mutu wathu ukunena kuti Ana “kweza mapemphero ndi mapembedzero mwa kulira ndi misozi.” Yesu anapemphera mokhudzika, kulira kwa kukulu ndi misozi. Madzulo ano ndikufuna kulankhula za kukhudzika mpemphero.
+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.
+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +
I. Koyamba, pemphero labodza koma lopempheredwa mokhudzika.
A chipentekositi ambiri ndi ma kalizimatiki amaganiza kuti kupemphera mofuula ndi kulira, motengeka ndi mokhudzika ndi zigawo zofunikira mpemphero. Amaganiza kuti kufuula ndi kulira zimatanthauza kuti Mzimu woyera ali mpempheromo, ndi zimene amachita akamayimba, akamamvera ulaliki, ndi akamachita chirichonse mtchalitchi. Kuteroku ndi kulakwitsa. Kutengeka kwa pakokha sikutanthauza chirichonse. Chikhonza kutichotsa mpemphero. Akhoza kukhala machitidwe a ziwanda.
Ndikupatseni chitsanzo cha m’Baibulo cha pemhero la bodza longotengeka. Eliya anatsutsana ndi aneneri a Baala. Anawauza kuti alirire kwa Baala tsiku lonse lathunthu, ndipo iyenso adzapemphera kwa Mulungu wa Israeli. Mulungu amene adzayankhe ndi moto adzaonetsa kuti ndi Mulungu weni-weni. Aneneri a Baala anapemphera mokhudzika ndi kutengeka m’pemphero lawo. Zikanaoneka ngati zabwino izi m’matchalitchi amasiku ano! “Anaitana pa dzina la Baala kuchoka m’mawa mpaka masana, nanena O Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wobvomereza. Ndipo anabvinabvina paguwa adalimanga” (1 Mafumu 18:26). Dzuwa litapendeka “ anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo kuti mwazi wao anali chuchuchu.” (1 Mafumu 18:28). Koma “panalibe mau, kapena wobvomereza, kapena wakuwamvera.” 1 Mafumu 18:29). Kenaka Eliya anapemphera pemphero lalifupi kwa Mulungu ndipo Mulungu anatumiza moto kuchoka ku Mwamba. Kutengeka kwa ziwanda, kudumpha-dumpha, kufuula ndi kulira ndi zina zotere, sizinawachitire ubwino aneneri onyenga. Kungodzimva kokhako sikutanthauza chilichinse.
Ndaona zongotengekazo kwa nthawi zambiri. Sizinachitire ubwino. Nthawi ina yake ndimalangiza mtsikana wina m’chipinda cholangizira, ndimayesa kumulozera kwa Kristu. Koma ankango lira ndi kunjenjemera. Samasiya kuchita zimenezi nditamufunsa. Anandiyankha kuti amalira chifukwa cha machimo ake, koma sanasunthe kuchoka pa kulirira kwa Yesu. Sanayang’ane ndi kuika maganizo ake pa Kristu. Sanapulumutsidwe. Kenaka anatuluka mu mpingo ndikupita m’moyo wa tchimo lozama.
Anthu ena amangotengeka. Amasweka mtima namangolira pa china chirichonse. Ndakukumbukiranso mtsikana wina amene amachita zimenezi. Samachita izi utatha ulaliki kapena pamene akulangizidwa kuti adalire Kristu ayi. Amangochita nthawi ina iriyonse. Amangopezeka akukhetsa misozi ndi kulira. Samakhazika maganizo ake pa Kristu, kapena tchalitchi, kapena Baibulo. Tsiku lina anamva chisoni. Anatsatira zimene amadzimva natuluka mu mpingo. Sindinamuonenso.
Kulira ndi kufuula sizitanthauza kuti chinthu ndi “cheni-cheni.” Sizipanga pemphero kukhala leni-leni. Kuyesa kudziriza kapena ku fuula sizitanthauza chirichonse. Mukamapemphera, nganizirani chimene mukupempherera. Mukhonza kupemphera ndi misozi kapena ayi. Yesu anaonetsa kukhudzidwa kwake m’munda wa Gethsemane. Anapemphera “ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” Koma samadzilirira. Misozi yake si napange pemphero likhale la bwino ayi. Misozi yake inatuluka m’pemphero. Inachokera mpemphero. Analirira kwa Mulungu mkuzingwa kwake, mkukanikizidwa ndi ululu, pamene machimo a mtundu wa anthu onse anaikidwa pa Iye. Kulira kwake kunachokera mkukhudzidwa kwake, ndi mtolo wake, ndi kunzunzika kwake. Chimodzimodzi inunso. Osamayesa kulira. Osamakonzekera kulira. Muzingopemphera. Mulungu akhoza kukutsogolerani mkulira, kapena ayi, koma monsemo lidzakhala pemphero leni-leni.
II. Kachiwiri, pemphero labodza lochitka mosakhudzika.
.Mapemphero ambiri amene akuchitika masiku ano simapemphero konse. Ndi zongolankhula za munthu, asati pemphero leni-leni lopita kwa Mulungu. Ndi mau chabe amene akungomveka bwino, akungomveka mwa chipembedzo-pembedzo, ndiwongotsatira dongosolo, opanda tanthauzo, osayang’a kwa Mulungu ndi ku mupempha china chake.
Ndakha ndikupita ku miyambo yomaliza maphunziro a ukachenjede ya mbiri. Koyambirila kwa mwambo kumayenera kukhale “mau oyamba” amayenera kuti azikha pemphero, koma sizikhala choncho. Munthu amango werenga mizire yochepa kuwalimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti akakhale anthu a bwino, ndikuti akakhale ndi moyo wa bwino. Palibe amene amayembekezera kuti Mulungu akhoza kuyankha kapena kusintha chinachake m’miyoyo yawo
Nthawi ina ndinapita ku Washington D.C., likulu la dziko lathu. Komeneko ndinakalowa mkachisi wa mkulu. Pulezidenti Reagan anali atangomwalira, ndipo amakonzekera za mwambo wa maliro ake. Kumeneko ndinamva wa mkulu wa nsembe akunema mau a “pemphero”. Komatu samapemphera nkomwe. Amangowerenga mau kuchokera mbuku. Basitu. Samamupempha Mulungu kuti achite china chake. Samayembekezeranso yankho. Anangolankhula mau pakuti ndizimene anayenera kuchita. Sanadzimve kuchoka mu mtima wake.
Yesu ananena ndi Mfarisi amene anpita ku Kachisai kukapemphera. Munthuyo anati, “Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opamba-pamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wa msonkho uyu; ndimasala chakudya kawiri pa sabata limodzi, ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndiri nazo.” (Luka 18:11,12). Samapempheratu apa. Sanamupemphe Mulungu chinachirichonse. M’malo mwake amamuuza Mulungu m’mene iye analiri wa bwino. Kristu anati anapemphera “ mwa iye yekha” (Luka 18:11). Sanaonetse ku khudzika. Sanapemphere kuchoka mu mtima mwake.
Kristu anawadzudzula a Farisi chifukwa cha mapemphero awo a bodza. Anati, “tsoka inu, alembi ndi Afarisi,onyenga! Pakuti mulanda nyumba za amasiye, ndi mwachinyengo mupemphera pemphero lalitali” (Mateyu 23: 14). Amapemphera pemphero lalitali kusonyeza kuti ndi woyera. Koma chimene amafuna ndikulanda nyumba ndi chuma cha azimayi okalamba. Cholinga chao chinali chomwech basi. Zonse zimene amachita kunali kungodzionetsera kuti aoneke ngati a bwino. Samapemphera kuchoka ku mitima yao. Mitima yao sinali yo londola.
Mukhonza kunena kuti, “Ine sindiri ngati amenewo” Koma kodi m’mapemphera mwa chinyengo, kumango werenga mau? Inenso ndachitapo. Munthawi ya ma mapemphero anu a mseri, kodi mumango tchula maina a anthu ndi zinthu zimene mukuzipempherera, mosaziganizira, mosapempha Mulungu kuti akupatseni mayankho? Kodi mwachitapo izi m’mapemphero a ku mpingo kwanu? Ine ndachitapo. Kodi mwapempherapo chifukwa mukuyenera kupempherera china chake – pakuti akusankhani kuti mupemphere? Mumasangalala kuti nthawi ya mapemphero yatha ndiye simuyenera kupempheranso. Limenero sirinali pemphero, leni-leni, anali mau ongolankhula chabe. Ndikuti, “Osakonzeratu mapemphero, apempherereni iwo!” Musanayambe mapemphero, mumupemphe kaye Mulungu kuti akuthandizeni kupemphera. Ndipo mukamapemphera pa gulu kapena panokha, muziganizira zomwe mukupempherera. Mukaganizira kwambiri za bvuto, ziri ngati kuti Mulungu sathandiza. Ganizirani za m’mene mufunira yankho lochokera kwa Mulungu. Kusala kudya kumathandizira pemphero, pakuti limakuthandizani kuonetsera Mulungu kuti simukucheza. Potolokerani kwa Mulungu m’pemphero lanu mupempheni Iye kuti akupatseni chimene mukupempha. Mukhonza kulira bwinolomwe m’kudzimva kwanu. Musadziletse. Mulungu wakukankhirani kumeneko. Nthawi zina simuyenera kulira. Osadzikakamiza kuti mpaka mulire. Pemphero sikuti limakhala labwino pokhapokha mwalira ayi – komanso silikhala labwino pamene simunalire ayi. Pemphero limakhala labwino Mulungu akakhalamo!
III. Kachitatu, pemphero leni-leni lokhudzika ndi losakhudzika.
Mutu wathu ukunena kuti Kristu anapemphera M’munda “ndi kulira kwa kukulu ndi misozi.” Koma nthawi zina pemphero leni-leni limene limalandira mayankho limachitika modzimva pang’ono mwinanso osadzimva. Ndinakuuzani za aneneri a Baala anapemphera kwa mulungu wao wa bodza. Tsopano ndikuuzeni m’mene Eliya anapempherera. Anati,
“Yehova Mulungu wa Abraham, Isake ndi Israeli, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu” (I Mafumu 18:36, 37).
Sizinalembedwe kuti Eliya analira. Sizinalembedwe kuti anadumphadumpha. Komanso sanadzicheke-cheke! Anangopemphera pemphero la chitsimikizo kwa Mulungu. Anapempha Mulungu kuti aonetsere kuti Iye ndi Mulungu weni-weni. Ndipo Mulungu anayankhadi pempherolo potumiza moto kuchoka kumwamba ni uotcha sembe ya Eliya. Anthu anati, “Yehova, ndiye Mulungu; Yehova ndiye Mulungu.” (I Mafumu 18:39). Pemphero lotsimikizika la Eliya, losachita mongotengeka, linatsutsana ndi aneneri a Baala. Pemphero leni-leni silichita kosoweka kuchita kudzimva. Limangosoweka kukhala ndi Mulungu!
Komabe nthawi zambiri kudzimva, chingakhale kukhetsa misozi, kumatsagana ndi pemphero leni-leni. Mukazindikira kuti muli ndi chosowa, ndichikhalidwe kuti muyambe kudzimva. Mukhoza kuyitana pa Mulungu mokhudzika, ndi kulira. Mukhonza kusweka mtima ndi kumupempha ndi misozi. Nthawi zambiri Baibulo limalumikiza misozi ndi pemphero. Woyimba adapemphera, “Imvani pemphero langa, yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga.” (Masalmo 39:12).
Mfumu Hezekiah anadwala matenda aku imfa. Hezekiya anapemphera kwa Mulungu. Anapemphera motani? Baibulo limati, “Nalira Hezekiya kulira kwakukuru.” (II Mafumu 20:3). Inde analira . Amafa ndithu. Analira mosweka mtima. Analira m’mapemphero ake. Kenaka mau a Ambuye anadza kwa mneneri Yesaya. Yesaya anati, bwerera nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, Ndapenya misozi yako: taona ndidzakuchiritsa.” (II Mafumu 20:5). “ Ndaona misozi yako.” Mulungu anona misozi ya Hezekiya. Pemphero lopempha. Ndipo Mulungu anayankha napulumutsa moyo wa mfumu.
Mu chipangano chatsopano, munthu wina anadza kwa Yesu. Mwana wake anali wodzazidwa ndi ziwanda. Yesu anamufunsa ngati akukhulupirira kuti mwana wake angathe kuchira. Pomwepo “atate amwana anafuula, nanena, ndikhulupirira, thandizani kusakhulipirira kwanga.” (Marko 9:24). Yesu anatulutsa ziwanda mwa mnyamata uja. Kawiri-kawiri uthenga uwu umagwiritsidwa ntchito posonyeza kuti amene ali wofoka mchikhulupiriro akhonza kuyankhidwa. “Thandizeni kusakhulupirira kwanga.” Komatu uthengau ukutinso atate “ analira” ndipo analankhula ndi Khristu “ ndi misozi munthuyu sanali m’modzi wa ophunzira. Si analinso munthu wotembenuka. Anali “m’modzi wa anthu a mkhamulo”, munthu wamba mkhamu la anthu. (Marko 9:17). Koma anadzanaye mwana wake kwa Yesu namulirira Iye ndi misozi.
Ndichifukwa chiyani munthuyu analirira kwa Yesu ndi misozi? Sanali kadaulo mpemphero ndipo sanali wotembenuka. Anayenera kulankhula ndi Yesu moteromo, pakuti anali ndi chosowa. Mwana wake anali wodzazidwa ndi ziwanda ndipo panalibe njira ina yotulutsira ziwandazo popanda Yesu. Munthuyu sanachite kudzirizira dala. Kuchoka mchosowa chake, kuchoka mkuzingwa kwake misozi inaturuka. Kumva chosowa, kuzindikira kuzingwa ndi kuperewera kwa chiyembekezo, kawiri-kawiri kumakufikitsa pa kulira ndi misozi. Analankhula mpemphero leni-leni, lakudzimva.
Izi zikutibweretsanso ku mutu wathu. Kristu analira m’munda “ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” Sikunali kulira kwa khanda. Sanali khanda longolira chirichonse. Anali munthu wa mkulu, woposa zaka makumi atatu. Nchifukwa chiyani analira? Chifukwa anakhudzika mu mtima mwake. Anamva tchimo la mzimayi ndi mzibambo wina aliyense liri pa Iye. Analingalira za imfa yapamtanda yowawitsa imene ayenera kufa nayo mawa lake, apo ayi palibe ndi m’modzi yemwe akadapulumuka. Kulemera kwa tchimo la munthu aliyense linai pafupi kumupha. Pakadapanda chisomo cha Mululngu akadafera m’munda momwe muja osakwanitsa kukafera pa mtanda. Kristu ananzunzika mumtima mwake. Ndipo anapemphera “kwakukulu ndi misozi.” Kunali kwachidziwikire nthawi ngati imeneyi. Chikanakhala chodabwitsa ngati sakana pemphera mosweka mtima. Yesu anapemphera “kwa kukulu ndi kulira.” Ndipo mutu wathu ukutiuza kuti “anayankhidwa” Mulungu anayankha pemphero lake namusungabe ndi moyo mpaka pa mtanda mawa lake. Mulungu anayankha “kulira kwakukulu ndi misozi” Yake.
Mkristu, ndikufunseni “mumapemphera molira ndi misozi?” Sindikunena pemphero lirilonse limene mugapemphere. Ndikufunseniso, kodi munapemherapo molira ndi misozi?” Ine ndachitapo, koma osati kawiri-kawiri. Kodi mumapemphera ndi mtolo wa zosowa, nimupempha Mulungu kuti akuyankheni – nthawi zina ndi kulira ndi misozi? Ngati simuchita, simuli ndi moyo wa pemphero wabwino. Ngati muli wotere, osasiya ndi kudikira kuti mpaka mapemphero anu atasintha. Izi sizimene Mulungu akufuna. Koma pempherani kwa Mulungu kuti akutakaseni ku zosowa zanu, kenaka mudzapemphera mokhudzika. Ngati mumasala zakudya, nthawi imene mwamva njala, mulingalire zimene mukupempherera. Tembenukirani kwa Mulungu ndi kupemphera.
Ena a inu munasochera. Simunamudalire Yesu. Ndikufunseni, “mumamva pemphero lanu tchimo lanu ndi kulira ndi misozi – pakanthawi kena?” Mumakhudzidwa ndi tchimo lanu? Kulira sindiye chindunji – chindinji ndi Yesu. Mudalireni kaya mukulira kapena ayi. “Koma ndikunena kuti, kodi mumadzimvera chisoni chifukwa cha tchimo la mumtima wanu?” Muyenera kutero, pakuti mtima wanu ndi “ wonyenga koposa” (Yeremiya 17:9). Pempherani kwa Mulungu kuti akuonetsereni tchimo la mumtima mwanu. Kenaka mupemphere kuti Mulungu akutengereni chifupi ndi Kristu.
Yesu ndi yankho la chosowa chanu. Ndipo ndi dipo la machimo anu. Anafa pa mtanda kulipira machimo anu onse, chingakhale machimo a mumtima. Anataya mwazi wake kubvundikira machimo anu ndi kuatsuka kwa muyaya. Anauka kwa a kufa kuigonjetsa infa ndi moyo, osati kwa Iye yekha, koma kwa inunso. Mukamudalira Yesu, mudzapulumutsidwa kwa muyaya. Mukafuna kulankhula nafe zokhudza kudalira Kristu, chonde fikani mudzakhale mizire iwiri yoyambirirayi. Amen.
MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.
(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”
Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo
Nyimbo yoimbidwa kumapeto wa ulaliki ndi Bambo Jack Ngann:
“Teach Me to Pray” (Albert S. Reitz, 1879-1966).
KALEMBEDWE KA MISOZI MPEMPHERO TEARS IN PRAYER ndi Dr. Christopher L. Cagan “Ameneyo, m’masiku a thupi lache anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kupulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa” (Ahebri 5:7). (Luka 22:44) I. Koyamba, pemphero la bodza koma lo pempheredwa mokhudzika, II. Kachiwiri, pemphero la bodza lochitika mosakhudzika, III. Kachitatu, pemphero leni-leni lokhudzika ndi losakhudzika, |