Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




CHILIMBIKITSO NDI CHENJEZO KU MSAUTSO ULIPO – NDI ULINKUDZA

ENCOURAGEMENT AND WARNING IN TRIBULATION –
NOW AND IN THE FUTURE

Ulaliki wolembedwa ndi Dr. R.L. Hymers, Jr.
Wosonkhanitsidwa ndi Dr. Christopher L. Cagan
Wolalikidwa pa Baptist Tabernade ku Los Angels.
Madzulo a tsiku la Ambuye, May 19,2019
A sermon written by Dr. R. L. Hymers, Jr.
with material by Dr. Christopher L. Cagan
preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord's Day Evening, May 19, 2019

“Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto: koma limbikani mtima; ndalilaka dziko la pansi Ine.” (Yohane 16:33)


Yesu anati, M’dziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto.” Liwu lakuti “chibvuto” likhonza kutanthauza kuti “Kupsinjika.” Tonse timapsinjika m’moyo mwathu. Koma nthawi yowawitsa yakupsinjika ikubwera. Chibvuto ndi nthawi ya zaka zisanu ndi ziwiri Khristu asanatsikire pa phiri la Azitona kulamulira dziko lonse mchiyero.Chigawo choyipitsitsa cha chibvuto chimenechi ndi zaka zitatu ndi theka zomalizira. Mu zaka zisanu ndi ziwiri Kristu asanabwerenso ku dziko la pansi, wokana Kristu adzalamulira dziko la pansi. Baibulo limaonetsa kuti yense amene adzakhale Mkristu mu nthawi imeneyi ya zaka zisanu ndi ziwirizi adzaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake.

Mtumwi Yohane anawona masomphenya a miyoyo ya a Kristu a chibvutochi Kumwamba. Anati,

“Ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo anaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu , ndi chifukwa cha umboni umene anali nao.” (Chibvumbulutso 6:9)

Kenaka analemba,

“Iwo ndiwo akutuluka mchisautso chachikuru, ndipo anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m’mwazi wa mwana wa nkhosa” ( Chibvumbulutso 7:14).

Zaka zisanu ndi ziwiri zimenezi zidzakhala zowawitsa kwa a Kristu kuposa nthawi ina iriyonse m’mbiri. Yesu anati,

“Pakuti pomwepo padzakhala masautso akuru, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” Mateyu 24:21).

Inde, kudzakhala mkwatulo. Baibulo limati,

Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwini yekha ndi mpfuu, ndi mau a mngelo wa mkuru, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m’mitambo, kukakumana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.” (I Atesalonika 4:16-17)

Koma tisaganize kuti lonjezano limeneri likutanthauza kuti sitikhala ndi mayesero lero lino ayi, ngakhale msautso wa ukuru usanafike M’malemba a mutu wathu, Yesu anati a Kristu adzakhala ndi chibvuto munthawi yonseyi.

“Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukhale nao mtendere. Mdziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto, koma limbikani mtima ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 16:33)

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

MA ULALIKI ATHU AKUPEZEKA MU MA FONI
ANU A M’MANJA TSOPANO.
PITANI KU WWW.SERMONSFORTHEWORLD.COM.
DAFANYANI BATANI LOBILIWIRA LOMWE LIRI NDI LIU LOTI “APP”
TSATIRANI MALANGIZO OTSATIRAWO.

+ + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + + +

Tiyeni ti lingalire zimene Yesu ananenaizi mosamalitsa. Ndiyamba kuthirirapo ndemanga chigawo cha chiwiri cha vesi limeneri, kenaka gawo loyamba, kenakanso gawo lomalizira.

I. Choyamba, “mdziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto.”

Yesu ananena izi kwa Ophunzira ake, ndipo izi zikukhudza a Kristu onse munthawi ino. Akristu adzakumana ndi mabvuto akuthupi. Mtumwi Paulo analemba motere,

“Ndipo kuti tingakwezeke koposa, chifkwa cha ukulu woposa wa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi….” (II Akorinto 12:7)

Izi zikuoneka ngati kuti ndi bvuto limene Paulo analinalo la mdiso lake. Ndichionetsero choti Akristu adzadutsa m’masautso amatenda akuthupi, kumva ululu ndi kumwalira. Sitingazembe matenda a m’thupi ndi ululu tikakhala Akristu.

Akristu adzadutsanso m’mayesero ndi msautso mdziko lathu lakugwa ndi lochimwa. Mtumwi Paulo ankalankhula za Akristu kukumana ndi

“….nsautso, kapena kupsinjika mtima, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi? Monga kwalembedwa, chifukwa cha Inu tirikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha” (Aroma 8:35-36)

Koma anasonyeza kuti chisautso chimenechi sichidza “tisiyanitsa ndi chikondi cha Kristu” (Aroma 8:35a).

“Mdziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto” (Yohane 16:33)

Atumwi onse anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chao mwa Kristu – kupatulako Yohane- yemwe ananyikidwa m’mafuta ogaduka, ndi kunzunzika ndi zilonda moyo wake wonse. Akristu mzaka zonsezi akhala akunzunzika chifukwa cha chikhulupiriro chao. Foxe’s Book of Martyrs ndi buku limene limanena za kunzunzika kwa a Khristu m’mbiri yadziko lapansi. Dr. Paul Marshall anati.

Mkati-kati mwa nkhalango za pakati pa Amereka….misasa ya ma China, mndende za ku Pakistani, mzipolowe za ku India, ndi ku midzi ya ku Sudan okhulupirira osawerengeka alipa kale dipo la chikhulupiliro chao (ibid, tsamba 160).

Ku Sudani a Khristu atengedwa ukapolo. Ku Iran akuphedwa. Ku Cuba akuikidwa m’ndende. Ku China akumenyedwa mpaka kufa. M’maiko pafupifupi 60 dziko lonse la pansi a Khristu akunyozedwa, kutukwanidwa, ndi kunyongedwa chifukwa cha chikhulupirilo chao. Akhristu 200,000,000 m’dziko lonse lapansi akukhala mwa mantha kuopa a sirikari. …. Mazana-mazana a Khristu akunzunzika chifukwa cha chimene anakhulupirila. (Pual Marshall, ph.D., Their Blood Cries Out, Word, 1997, back jacket).

Chingakhale kuno kwa a zungu, a Kristu eni-eni akunyozedwa, ndi anthu opanda chipembedzo. Chikristu ndi Baibulo zikunyozedwa m’makalasi a ku makoleji. A Kristu ambiri akumanidwa zitukuko, ndi ena akuchotsedwa ntchito chifukwa chofuna kukapemphera ku ma tchalitchi kwao pa tsiku la Ambuye. Chingakhale anthu osapemphera ndi a kristu ena ofoka, akumanyoza a Kristu odzipereka. Monga m’mene Yesu ananenera,

“Mdziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto” (Yohane 16:33)

II. Chachiwiri, “izi ndanena kwa inu, kuti mukhale ndi mtendere mwa Ine.”

Ili ndi lonjezo kwa iwo ali “mwa Khristu” “Mwa Ine” Iye ndi chiyambi cha mtendere wa mu mtima. Yesu anati.

“Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa…” (Yohane 14:27)

Pamene munthu walandira Khristu, amakhala ndi mtendere wokhazikika, umene ena m’dziko lapansi alibe.

Munthu amene ali “mwa” Khristu, ndikuti amapereka mabvuto ake kwa Mulungu m’pemphero, amakhala ndi mtendere wodabwitsa, umene Baibulo limautcha “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse” (Afilipo 4:7). Dziko silingamvetse chifukwa chimene a Kristu amalolera kumangidwa, kunzunzika, kuikidwa mndende, ndi kuphedwa – pakuti oterewa ali m’mayiko ambiri dziko lonse lapansi usiku uno.

Mtendere umenewu siukutanthauza kuti a Kristu alibe nkhondo ya mumtima, ndi mabvuto osiyana-siyana. Ma evangeliko ambiri ku Amereka ndiwotanganidka ndi kuchitabwino, chuma, kupambana, ndi zisangalaro zosiyan-siyana. Moti ziphunzitso ngati izi zimaoneka ngati zopusa, Akristu a ku China akuphedwa mozondotsedwa chifukwa cha chikhulupiriro chao, a Kristu a ku Cuba akhala mndende zaka zisanu osaweruzidwa, ndipo a Kristu a ku Iran akuphedwa chifukwa chokhulupirira Yesu.

Akristu a m’maiko okwera kumene akutha kuzindikira tsopano zimene Yesu amanena kuti “izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere.” (Yohane 16:33). Ndikukhulupirira kuti akutha kudziwa kuti mtendere umenewu ndi wa mu mtima, pozindikira kuti machimo awo akhululukidwa, ndikuti Mulungu amawasamalira.

Ndiwerenga II Akorinto 11: 24-28. Mvetserani pamene ndikukuuzani zomwe zinamuchitikira Mtumwi Paulo. Iye anati,

“Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m’kuya tsiku limodzi usana ndi usiku; paulendo kawiri-kawiri, moopsya mwache mwa mitsinje, moopsya mwache mwa olanda, moopsya modzera kwa a mtundu watundu wanga, moopsya modzera kwa a mitundu, moopsya m’mudzi, moopsya m’chipululu, moopsya m’nyanja, moopsya mwa abale onyenga; m’chibvutitso ndi mcholemetsa, m’madikiro kawiri-kawiri, mnjala ndi ludzu, m’masalo a chakudya kawiri-kawiri, mchisanu ndi umariseche. Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chilabadiro cha mipingo yonse.” (II Akorinto 11:24-28)

Paulo amaneneranji za mtendere chonsecho akudutsa m’mabvuto ngati amenewa? Paulo anayankha funsoli pa Afilipo 4:6,7.

“Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mterendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu/” (Afilipo 4:6-7)

“Paulo anadutsa mzokhoma zambiri koma amalankhulabe za “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse.”

III. Chachitatu, “koma limbikani mtima ; ndalilaka dziko lapansi Ine”

Mukhonza kukhala ndi nkhawa ngati mungakwanitse kudutsa m’mayesero ndi m’manzunzo ngati amenewa. M’masukulu achinyamata akunyoza Baibulo ndi kulinenera zinthu za chipongwe. Inu nkumati, “ Kodi ndingakwanitse, ndikupitirira kukhala mKristu?” Kodi ndirimba pamene anthu akundiukira? “Kodi ndingakwanitse pamene mantha akundigwira – ndikuoneka ngati ndiribe chikhulupiriro chokwanira?”

Masiku ano aKristu eni-eni akunyozedwa kuti achita misala. Anthu adzanena kuti mwaonjeza za Yesu-zi. Akuti mukamusiya Kristu ndi pamene muyambe kusangalala. “ Sipafunikanso kunyamula mtanda. Sipafunikanso kunzunzika kapena kumva zowawa,” amati. “Ziiwareni zimenezo. Khalani ngati m’mene ife tiriri. Amakukakamizani kuti muchite zimenezi. Monga m’mene Yesu ananenera, “Mdziko la pansi mudzakhala nacho chibvuto.”

Koma Kristu akuti, “limbikani mtima ndalilaka dziko lapansi” Mvetserani pamene ndi kuwerenga Aroma 8:35-39.

“Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kunzunza, kapena njala, usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi? Monganso kwalembedwa , chifukwa cha Inu tiri kuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha. Koma m’zonsezi, Ife tilakatu mwa Iye amene anatikonda. Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu ziri nkudza, ngakhale zimphamvu, ngakkhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chirichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu , chimene chiri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:35-39)

Mukadza kwa Kristu, amakulandirani zothodwa zanu zonse. Amakugwirizizani osakutayani konse. Mukadza kwa Kristu, inu simuyenera kumgwiriziza Iyeyo. Iyeyo ndi amene amagwiriziza inu! Kuyambira pamene munatembenuka mmtima, ndinu wotetezedwa kwa muyaya mwa Kristu. Chokhacho chakuti kuli anthu 200 miliyoni m’maiko okwera kumene amene akonzeka kunzunzika chifukwa cha chikhulupiriro chao ndi chitsimikizo chakuti Kristu akugwiriziza omutsatira ake, ndipo sadzalola kuti awonongeke popanda chiyembekezo chokalowa kumwamba. Idzani kwa Kristu, adzachita zonse zokupulumutsani, ndi zonse zokusungani! Monga m’mene anayimbira bambo Ngann tisanayammbe ulalikiwu,

Moyo wodalira pa mayankho a Yesu
   Sindingathe, sindingathe kuthawira kwa adani ake
Amene moyo yawo udzapita ku gehena
   Sindidzamsiya konse.
(“Maziko okhazikika,” ‘K’ in Rippon’s ‘Nyimbo za chitsitsimutso,’ 1787).

Mutu wa ulaliki uwu ndi “Chilimbikitso ndi Chenjezo ku Msautso – Ulipo ndi ulinkudza.” Ndakupatsani chilimbikitso madzulo ano. Koma ndiyenera kukupatsani mau a chenjezo. Mabvuto onse amene tingadutsemo tsopano ndiwochepa kulinganiza ndi amene akudutsamo anzathu m’maiko ena. A Kristu a m’maiko okwera kumene akumenyedwa, kuikidwa mndende, kunzunzudwa ndi kuphedwa chifukwa chakukhulupirira Yesu. Moyo wathu kuno ku Amereka ndi wa manyado polinganiza ndi anzathuwo kumeneko. M’zaka zikubwerazi zidzakhala zobvuta kwambiri kukhala m’Kristu kuno. Kupsinjika kudzakula kwambiri. Mudzataya ntchito, nyumba, ndi ndalama chifukwa chokhala m’Kristu wene-weni. Zikuchitika m’maiko ena pakali pano. Anzanu ndi abale anu adzakuukirani. Polankhula za chisautso chimenechi, Yesu anati, “Ndipo mbale adzapereka mbale wache kuti amuphe, ndi atate mwana wache; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawapha. Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa” (Marko13:12,13). Zikuchitika m’maiko ena pakali pano. Musadabwe ngati anthu akukaneni zaka zisanu ndi ziwirizi zisanafike.

Mneneri Yesaya anati, “Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akabvalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m’dziko la mtendere udzachita bwanji mkudzikuza kwa Yordano?” (Yeremiya 12:5). Inde mukudutsa mu msautso tsopano. Koma ngati simungathe kupirira ndi lero, mudzatani zinthu zikadzafika pobvuta kwambiri? Ngati simungakhale moyo wa chikristu munthawi ya zosangalatsa ino, mudzatani pamene mafunde adzaomba? Ndikukulimbikitsani kuti mukhale a Kristu olimba tsopano. Mukatero tsopano, mudzakhala olimba nthawi imeneyo. Ndinkachiganizira ichi ndikadali m’Kristu watsopano pamene ndi nkawerenga buku la Mbusa Richard Wurmbrand, Kunzunzika chifukwa cha Kristu. Sirinangokhala buku lowerenga chabe. Linasintha moyo wanga. Kukhala m’Kristu sichinthu chongosangalatsa. Chikhonza kukhala chinthu chobvuta. Ndi chobvutadi. Inde, “limbani mtima” (Yohane 16:33). Komanso werengerani mtengo wache (onani Luka 14:28). Mudzalandira mphotho yake, pakuti mudzakhala ndi Kristu nthawi zonse.

Tsopano ndifuna ndilankhule ndi osochera amene muli muno usiku uno. Yesu amakukondani. Anafera pa mtanda kulipira dipo la machimo anu. Anakhetsa Mwazi Wache kutsuka machimo anu. Anadzuka m’manda kukupatsani moyo. Mukango Mukhulupirira, mudzapulumuka kwa muyaya. Koma kumudalira Yesu simau ochepa chabe. Kumudalira Yesu zitanthauza kumudalira Yesu. Inde, kudzakhala nthawi zowawa. Inde, mungathe kunzunzika. Koma lidzakhala dipo loyenera. Mudzamudziwa Yesu. Mudzakhala ndi Kristu kwa muyaya ngati mutamudalira Iye. Ngati mukufuna kulankhula limodzi nane pa za kumudalira Yesu, chonde bwerani mudzakhale m’mizere iwiri yoyambirirayi. Amen.


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo

Nyimbo usanayambe ulaliki ndi Bambo Jack Ngann
“Maziko okhazikika” (‘K’ in Rippon’s ‘nyimbo za chitsitsimutso,’ 1787).


KALEMBEDWE KA

CHILIMBIKITSO NDI CHENJEZO LA MSAUTSO –
ULIKO NDI ULINKUDZA

ENCOURAGEMENT AND WARNING IN TRIBULATION –
NOW AND IN THE FUTURE

Ulaliki wolembedwa ndi Dr. R.L. Hymers, Jr.
Wosonkhanitsidwa ndi Dr. Christopher L. Cagan

“Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto: koma limbikani mtima; ndalilaka dziko la pansi Ine.” (Yohane 16:33)

(Chibvumbulutso 6:9; 7:14; Mateyo 24:21; I Atesalonika 4:16-17)

I.   Choyamba, “mdziko lapansi mudzakhala chibvuto,”
II Akorinto 12:7; Aroma 8: 35-36.

II.  Chachiwiri, “Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa
Ine mukhale nawo mtendere,” Yohane 14:27;
II Akorinto 11:24-28; Afilipo 4:6-7.

III. Chachitatu, “limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi,”
Aroma 8:35-39; Mariko 13:12, 13; Yeremiya 12:5; Luka 14:28.