Print Sermon

Cholinga cha tsamba ili ndi kupereka ma ulaliki a ulere olembedwa komanso a mkanema kwa a busa mdziko lonse la pansi makamaka maiko okwera kumene, komwe kuli ma sukulu a Baibulo ochepa kapena kulibiretu.

Maulaliki awa olembedwa komanso a m’ma video akupezeka pafupifupi m’ma kompyuta 1,500,000 m’maiko 221chaka chilichonse pa www.sermonsfortheworld.com. Anthu zikwi-zikwi amaonera kanema wa pa YouTube, koma kenaka amasiya YouTube ndikubwera ku website yathu. You Tube imawalondolera anthu ku website yathu. Maulaliki olembedwawa akupezeka mzilankhulo 46 mu makomputa 120,000 mwezi uli wonse. Maulalikiwa alibe chiletso, kotero alaliki akhoza kuagwiritsa ntchito mosafuna chilolezo. Chonde sindikizani apa kuti mudziwe m’mene mungaperekere thandizo la mwezi ndi mwezi lomwe lingathandize kwakukulu pofalitsa uthenga wa bwino kudziko lonse la pansi.

Mukafuna kulembera Dr. Hymers nthawi zonse muuzeni dziko limene mukukhala, apo ayi sangakuyankheni. E-mail ya Dr.Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net.




KRISTU YESU MWINI

JESUS CHRIST HIMSELF
(Chichewa – A Language of Malawi)

Wolemba Dr. R. L. Hymers, Jr.

Uthenga wolalikidwa pa Baptist Tabernacle ku Los Angeles
m’mawa wa tsiku la Ambuye, April 12, 2015
A sermon preached at the Baptist Tabernacle of Los Angeles
Lord’s Day Morning, April 12, 2015


Ili ndi tsiku lopambana kwa mkazi wanga pamodzi ndi ine. Tonsefe timasangalala kuti ndi tsiku lomwe tinabadwa lero. Tsiku leni-leni, April, 12, nditsiku la makumi asanu ndi awiri ndi mphambu zinayi langa. Leronso ndi tsiku limene ndikukumbukira kuti ndakwanitsa zaka makumi asanu ndi mphambu zisanu ndi ziwiri chiitanidwireni mu utumiki mchaka cha 1958. Koma, koposa zonse, ili ndi tsiku lopambana la mpingo wathu. Zaka makumi anayi apitawo ndinayamba mpingo uno ndi achinyamata asanu ndi m’modzi kapena asanu ndi awiri m’kachipinda mwanga, mkadera ka Westwood ndi Wilshire Boulevard, midada yochepa chabe kuchokera pa UCLA, University yotchuka ya West Los Angeles. Ndi anthu awiri okha amene akanalipo mpaka lero lino, Bambo John Cook ndi ine. Mwa chisomo cha Mulungu John ndi ine tili muno m’mawa uno patatha zaka makumi anayi. Yesu alemekezeke!

Mpingo uno wadutsa zaka makumi anayi a mayesero. Monga ana a Israeli anatha zaka makumi anayi mchipululu, koteronso mpingo uno wadutsa m’zokhoma zambiri, mabvuto ambiri, komanso zotsutsana nafe. Ndilankhula zambiri za izi madzulo ano. Koma tsopano ndife mpingo waukulu wolalikira uthenga wabwino malo akulu ku Los Angeles. Ndipo tikudziwa, kuti m’zovuta zathu zonse, Mulungu wakhala nafe ndipo watigonjetsera ndim’mene tikusangalalira lero, kukumbukira kuti mpingo wathu watha zaka makumi anayi! Yesu alemekezeke!

M’busa Roger Hoffman analankhula pa mapemphero a usiku wathawu. Alankhulanso usiku uno pachisangalaro chathuchi. Koma Mbusa Hoffman wakana nditamupempha kuti alalikire m’mawa uno. Anati, “Dr. Hymers, ndikufuna ndikumveni mukulalikira Lamulungu m’mawa.” Ndiye pamene ndimapemherera choti ndilankhule, ndinatsogozedwa kuti ndibwereze uthenga umene ndinalalikirapo ku Mpingo wa Baptist wina m’mwezi wa August, 2010. Chonde tsekulani nane limodzi buku la Aefeso, chaputala cha chiwiri. Ndi tsamba 200 mbuku la Chichewa cha kale. Imilirani pamene tikuwerenga Aefeso 2:19, 20.

“Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, koma muli a mudzi omwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa pangondwa” (Aefeso 2:19, 20).

Khalani pansi.

Apa m’mavesi amenewa Mtumwi Paulo akutiuza kuti mpingo ndi nyumba ya Mulungu. Ndiye akutiuzanso kuti mpingo anamangidwa pa maziko a atumwi ndi aneneri, koma Yesu mwini ndiye “ndi mwala wa pa ngodya.” Dr. J. Vernon McGee anati izi zitanthauza “kuti Kristu ndi thandwe pamwe mpingo unamangidwapo” (Thru the Bible, Volume V, Thomas Nelson, p. 241; po tanthauzira Aefeso 2:20). Dr. A. T. Robertson anati, “akrogōniai…mwala weni-weni wa maziko” (Word Pictures, Broadman, 1931; pa matanthauzo a Aefeso 2:20). Yesu Kristu Mwini ndi maziko a ntchito zathu zonse, ndi miyoyo yathu yonse. “Yesu Kristu Mwini” ndiye maziko eni-eni a mpingo wathu. Ndasankha mau emene ali pa mapeto pa Aefeso 2: 20 ngati mutu wathu m’mawa wuno.

“Kristu Yesu Mwini” (Aefeso 2:20).

Kristu Yesu Mwini ndiye mutu wa ulaliki wathu. Chikhulupirilo cha chi Kristu sikanthu kabwino koposa Kristu Yesu Mwini. Sanakhaleko ndipo sadzakhalako wofana ndi Yesu Kristu. Ndi wodabwitsa mu mbiri ya munthu. Kristu Yesu Mwini ndi Mulungu-munthu. Kristu Yesu Mwini anatsika kuchoka kuMwamba ndi kukhala pakati pa anthu.Kristu Yesu Mwini ananzunzika, anakhetsa mwazi ndikufa chifukwa cha machimo athu. Kristu Yesu Mwini anauka kwakufa kuthupi kutilungamitsa. Kristu Yesu Mwini anakwera kukakhalanso kudzanja lamanja la Mulungu kukatipembedzerera. Ndipo Kristu Yesu Mwini adzabweranso kudzakhazikitsa Ufumu wake pansi pano kwa zaka chikwi…. Uyu ndi Kristu Yesu Mwini! Imani tiyimbe kolasi imeneyi!

Yesu yekha, ndimuone
   Yesu yekha, palibe wopulumutsa Iye,
Ndi nyimbo yanga ndidzaimba-
   Yesu! Yesu yekha
(“Yesu Yekha, Ndimuona” wolemba Dr. Oswald J. Smith, 1889)

Khalani pansi.

Nkhani ya Kristu Yesu Mwini ndi yozama kwambiri, ndi yakuya, ndi yofunikira mwakuti sitingathe kuyilongosola mu ulaliki umodzi. Tikhoza kungokhudza mitu yochepa yokha m’mawa uno yokhudza Kristu Yesu Mwini.

I. Choyamba, Kristu Yesu Mwini ndi wonyozedwa ndi wokanidwa ndi mtundu wa anthu.

Mlaliki mneneri Yesaya ananena momveka kuti,

“Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa, ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitimamulemekeza.” (Yesaya 53:3)

Dr. Torrey anati, “Kulephera (kukhala) ndi chikhulupiriro mwa Yesu Kristu si tsoka lokha ayi, koma ndi tchimo, tchimo lolilitsa, tchimo loopsa, tchimo loipitsitsa” (R.A. Torrey, D.D., How to Work for Christ, Fleming H. Revell Company, n.d., p 431). Mneneri Yesaya analongosola za tchimo lonyoza ndi kukana Kristu, kunyozera kwa mumtima limene limapangitsa anthu otayika kubisa nkhope zawo kwa Kristu. Chitsimikizo cha kulephera kwa munthu nkwakuti amaganiza pang’ono za Kristu Yesu Mwini. Chitsimikizo chakuti munthu wotayika ayenera chilango cha muyaya kunyanja ya moto nchakuti amachitira dala mwachizolowezi kubisa nkhope zawo kwa Iye.

.Mchikhalidwe chosatembenuka anthu ananyoza Kristu Yesu Mwini. Mchikhalidwe chawo cholephera, salemekeza Kristu Yesu Mwini. Pokhapokha mutabayidwa mchikumbumtima chanu, pokhapokha mutadzimva kutsutsidwa ku machimo anu, pokhapokha mutadzimva kuti mtima wanu ndi wakufa pa Mulungu, mudzapitilira kunyoza ndi kukana Kristu Yesu Mwini.

Mumpingo mwathu timaona zimenezi zikuchitika mkachipinda kofunsira atatha maulaliki. Timamva anthu akunena zinthu zambiri. Amalankhula za ma vesi a m’Baibulo. Amalankhula zoti “ azindikira” Amatiuza a m’mene akumvera za izi kapena izo. Amatiuza m’mene anamvera ndi zomwe anachita. Amamaliza ponena kuti, keneka ndinadza kwa Yesu.” Basi! Sanganene liu lonena za Yesu! Alibe choti anganene za Kristu Mwini! Kodi angapulumutsidwe bwanji?

Chiphona Spurgeon anati, “Pali mchitidwe pakati pa anthu wo musiya Kristu Mwini kuchoka ku uthenga wabwino” (C. H. Spurgeon, Around the Wicket Gate, Pilgrim Publications 1992 reprint, p. 24).

Kungodziwa m’mene mungapulumutsidwire sizingakuthandizeni! Kuphunzira zambiri za Baibulo sikungakupulumutseni! Kungomva maulaliki ambiri sikungakupulumutseni! Kumva chisoni za machimo anu sikungakupulumutseni! Sizinapulumutse Yudasi, sichoncho? Kongodzipereka chabe sizingakupumutseni! Misozi yanu singakupulumutseni! Palibe chimene chingakuthandizeni pokha-pokha mwatsogozedwa kusiya kunyoza ndikukana Yesu Kristu – pokha-pokha mwakankhikira kwa Kristu Yesu Mwini! Imbaninso!

Yesu yekha, ndimuone
   Yesu yekha, palibe wopulumutsa Iye,
Ndi nyimbo yanga ndidzaimba-
   Yesu! Yesu yekha

Mukhoza kukhala.

II. Chachiwiri, Kristu Yesu Mwaini ndi phatha la Baibulo lonse.

Kodi chingakhale chopanda nzeru kukukuzani kuti Kristu Yesu Mwini akhale pakati pa malingaliro anu? Ayi, sikuti nchopanda nzeru. Chifukwa chiyani, ganizirani ichi, Kristu Yesu Mwini ndiye mutu waukulu mu Bibulo lonse – kuyambira ku Genesis mpaka chivumbulutso! Yesu atauka kwakufa anakumana ndi ophunzira ake awiri akuyenda panjira ya ku Emaus. Zimene ananena kwa iwo nchimodzi-modzinso lero lino.

“Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri! Kodi sanayenera Kristu kumva zowawa izi, ndikulowa ulemerero wake? Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo, m’malembo onse zinthu za Iye Yekha.” (Luka 24:25-27)

Kuchoka m’mabuku asanu a Mose, kumanso Baibulo lonse lathunthu, Kristu analongosolera iwo, “M’malembo onse zinthu zolankhula za Iye.” Kodi chikonzero chikanakhala chotani? Mutu wa ukulu wa Baibulo lonse ndi Kristu Yesu Mwini! Pakuti Kristu Yesu Mwini ndiye mutu waukulu m’baibulo, kodi si cha nzeru kuti Kristu Yesu akhale mutu wa nkhani m’maganizo ndi m’moyo wanu? Ndikuti muganizire mozama m’mawa uno za Kristu Yesu Mwini! Imbani!

Yesu yekha, ndimuone
   Yesu yekha, palibe wopulumutsa Iye,
Ndi nyimbo yanga ndidzaimba-
   Yesu! Yesu yekha.

Ndimakhulupirira kuti kudziwa Kristu Yesu Mwini, m’kutembenuka kweni-kweni, ndiye chinthu chofunikira kwambiri chimene chingachitike kwa inu. Ngati mumadaliradi Kristu Yesu Mwini mudzasoweka uphungu wochepa kwambiri. Ndimakhulupirira kumdziwa Kristu Yesu Mwini zeni-zeni osadaliranso kumapatsidwa ma uphungu a chi Kristu! Munthu akamudziwa Kristu, mkutembenuka kweni kweni, adzapeza kuti Kristu,

“…amene anayesedwa kwa ife nzeru, ndi chiyero, ndi chombolo” (1 Akorinto1:30).

Titasiya “kumangopanga Zisankho za pa ife tokha” m’mipingo mwathu, ndikuonetsetsa kuti anthu anatembenukira kwa Kristudi, zikanachotsa kudalira ma uphungu amene amachitika m’mipingo masiku ano! Muloleni Kristu Yesu Mwini akhale mlangizi! Imbani!

Yesu yekha, ndimuone
   Yesu yekha, palibe wopulumutsa Iye,
Ndi nyimbo yanga ndidzaimba-
   Yesu! Yesu yekha.

III. Chachitatu, Kristu Yesu Mwini ndi chiyambi, chinthu cha pa phata, pamtima peni-peni pa Uthenga wa bwino.

M’neneri Yesaya analankhula za Kristu Yesu Mwini ngati pamtima pa uthenga wa bwino,

“Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda mnjira yense m’njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anayika pa Iye mphulupulu ya ife tonse” (Yesaya 53:6).

“Yehova anayika pa iye mphulupulu zathu zonse.” Infa ya chigonjetso, ya Kristu, m’malo mwanu kulipira dipo la mkwiyo wa Mulungu m’malao mwanu – apa ndiye pa mtima pa uthenga wa bwino! Ndi Kristu Yesu Mwini kulandira machimo nkuyika pa Iye Mwini mumdima wa Getsemani. Anali yenkha m’Munda anati,

“Moyo wanga uli wa chisoni chambiri kufikira infa” (Marko 14:34).

Ndi Kristu Yesu Mwini amene,

“pokahala Iye mchipsinjo….ndi thukuta….likhala ngati madontho akuru a mwazi alinkugwa pansi” (Luka 22:44).

Ndi Kristu Mwini amene anagwidwa m’munda wa Getsemani. Ndi Kristu Yesu Mwini amene anam’dudulizila pamaso pa akulu a nsembe, anamupanda kumaso, anamunyoza namuchititsa manyazi. Anamulavulira malovu kumaso Kristu Yesu Mwini! Anam’mwetura ndevu zake Kristu Yesu Mwini! Ndi Kristu Yesu Mwini amene anatengedwera kwa Pilato, anakwapulidwa ku msana ndi shamboko, namveka chisoti cha minga, magazi akutuluka kumaso kwa nkhope Yake yodalitsika Kristu Yesu Mwini, kupandidwa kumaso kwake kosathaso kumuzindikira.

“Ndi nkhope yache… yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ache kupambana ana a anthu” (Yesaya 52:14).

“Ndipo ndi mikwingwirima yache ife tachiritsidwa” (Yesaya 53:5).

Ndi Kristu Yesu Mwini amene anatengedwa kuchoka ku bwalo la Pilato, nakoka Mtanda Wake ulendo wa kumalo opachikidwira. Anali Kristu Yesu Mwini amene anakhomedwa ndi misumali ku mtengo wotembeleredwa uja. Anali Kristu Yesu Mwini amene ananzunzika asati chifukwa cha misumali imene inalowa m’manja ndi m’mapazi Yake – koma ananzunzika kwambiri pamene Mulungu anati “anayika pa Iye mphulupulu ya infe tonse.” (Yesaya 53:6). Kristu Yesu Mwini “anasenza machimo athu mthupi mwake pa mtengo” (1 Petro2:24). Dr. Watts anati,

Onani, kuchokera m’mutu Wake, manja Ake, mapazi Ake
   Chisoni ndi chikondi zitsika:
Ndani akanakwanitsa chikondi chitere
   Kuvala chisoti cha minga?
(“When I Survey the Wondrous Cross,” Isaac Watts, D.D., 1674-1748).

Imani tiyimbe kolasi yathu!

Yesu yekha, ndimuone
   Yesu yekha, palibe wopulumutsa Iye,
Ndi nyimbo yanga ndidzaimba-
   Yesu! Yesu yekha.

Mukhoza kukhala.

IV. Chachinayi, Kristu Yesu Mwini ndi chiyambi cha chimwemwe chosatha.

Anatsitsita thupi la Yesu pamtanda nakaliika mbanda amene atsekapo ndi chimwala. Koma tsiku la chitatu, Anauka kwakufa! Nadza kwa Ophunzira nati, “Mtendere ukhale pa inu” (Yohane 20:19).

“Ndipo pamene ananena ichi, anaonetsa anaonetsa iwo manja ache ndi nthiti zache.” Pamenepo akuphunzira anakondwera pakuona Ambuye.”

“ Pamenepo akuphunzira anakondwera pakuona Ambuye”. (Yohane 20:20) Kristu Yesu Mwini anawapatsa mtendere “ atamuona Ambuye.” Simungadziwe mtendere, ndi chimwemwe cha Ambuye, pokhapokha muli ndi Kristu Yesu Mwini!

Oo, ndikukuuzani m’mawa uno – ndikutha kukumbukira nthawi imene ndina dalira Kristu Yesu Mwini! Inali nthawi yopambana! Ndinathamangira kwa Iye.Mwina ndinene kuti Iye ndi amene anathamangira kwa ine. Machimo anga anatsukidwa ndi mwazi Wake wodabwitsa! Ndinakhalanso wa moyo chifukwa cha Mwana wa Mulungu! Imbano kolasi ija!

Yesu yekha, ndimuone
   Yesu yekha, palibe wopulumutsa Iye,
Ndi nyimbo yanga ndidzaimba-
   Yesu! Yesu yekha.

Khalani pansi.

Idzani kwa Krisru Yesu Mwini! Musamusiye mpulumutsi wa moyo wanu. Musamusiye Yesu mu umboni wanu. Musachite chime Spurgeon “ mchitidwe wosauka…. Kumusiya Kristu Mwini muuthenga wabwino.” Ayi! Ayi! Idzani kwa Kristu Yesu. Vetselani mau awa pamene ndi kuyimba.

Monga m’mene ndiliri
   Koma mwazi wanu unakhetsedwera ine,
Kuti ndidze chifupi nanu,
   O mwana wankhosa wa Mulungu, Idzani! Idzani!
(“Just As I Am,” Charlotte Elliott, 1789-1871).

Yesu anafera pa mtanda kulipira dipo la machimo anu. Yesu anakhetsa Mwazi wake woyera kukutsukani ku machimo onse. Idzani kwa Yesu. Mdalireni Iye Adzakupulumutsani ku machimo onse. Amen.


MUKAFUNA KULEMBERA DR.HYMERS MUYENERA KUTCHULA DZIKO LIMENE MUKULEMERA APO AYI SADZATHA KUYANKHA KALATA YANU. Ngati maulaliki awa akudalitsani tumizani e-mail kwa Dr. Hymers ndikumuuza, koma nthawi zonse tchulani dziko limene mukulembera. E-mail ya Dr. Hymers ndi rlhymersjr@sbcglobal.net dafanyani apa. Mukhoza kumulembera Dr. Hymers mchilankhulo chirichonse, koma muyesetse Mchigerezi ngati mungathe. Ngati mukufuna kulembera Dr. Hymers pa positi, keyara yake ndi P.O. Box 15308, Los Angels, CA 9001. Mukhoza kuimba foni pa (818) 352-0452.

(MAPETO A ULALIKI)
Mukhoza kuwerenga ma ulaliki a Dr. Hymers sabata iriyose pa intaneti iyi
www.sermonsfortheworld.com,
dafanyani “Maulaliki mchichewa.”

Maulaliki awa si oletsedwa. Mukhoza kuagwiritsa ntchito kopanda kufuna chilorezo kwa
Dr. Hymers. Komabe, maulaliki a mkanema ya tchalitchi lathu ngofunika kuagwiritsa
ntchito potenga chilorezo

Mau owerengedwa ulaliki usanayambe ndi Bambo Abel Prudhomme: Yesaya 53:1-6.
Nyimbo yoyimbidwa ulaliki usanayambe mchizungu:
“When Morning Gilds the Skies” (Yotanthauzidwa kuchoka ku chi
German ndi Edward Caswall, 1814-1878).


KALEMBEDWE KA

KRISTU YESU MWINI

JESUS CHRIST HIMSELF

Wolemba Dr. R. L. Hymers, Jr.

“Kristu Yesu Mwini” (Aefeso 2:20).

I.   Choyamba, Kristu Yesu Mwini ananyozedwa ndi kukanidwa ndi mtundu wa anthu. Yesaya 53:3.

II.  Chachiwiri, Kristu Yesu Mwini, ndiye phata la mutu wa Baibulo lonse,
Luka 24:25-27; I Akorinto 1:30.

III. Kristu Yesu Mwini, chiyambi, chinthu cha paphata pa mtima peni-peni pa Uthenga wa bwino. Yesaya 53:6; Mariko 14:34; Luka 22:44;
Yesaya 52:14; 53:5; I Petro 2:24.

IV. Chachinayi, Kristu Yesu Mwini ndi chiyambi chokhacho cha mtendere
wosatha. Yohane 20:19, 20.